Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 16, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lanena Kuti Silisintha Chigamulo Chake Choti M’bale Mmodzi ndi Alongo Awiri Azitsatira Malamulo Ena ali Kunyumba

Khoti la ku Russia Lanena Kuti Silisintha Chigamulo Chake Choti M’bale Mmodzi ndi Alongo Awiri Azitsatira Malamulo Ena ali Kunyumba

Pambuyo pounikiranso mlandu wa M’bale Aleksandr Prianikov komanso Mlongo Venera ndi Darya Dulova, Khoti la mumzinda wa Karpinsk lapereka chigamulo chake pa 15 July 2021, kuti silisintha zoti m’baleyu ndi alongowa azitsatira malamulo ena ali kunyumba. Abalewa akapanga apilo chigamulochi. Koma panthawiyi sakufunikira kupita kundende.