Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 20, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lasintha Chigamulo cha Mlongo Larisa Artamonova

Khoti la ku Russia Lasintha Chigamulo cha Mlongo Larisa Artamonova

Pa 20 April 2021, khoti lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda linasintha chigamulo chimene chinaperekedwa kwa Mlongo Larisa Artamonova choti apereke chindapusa cha ndalama zokwana madola 135 a ku America. Khotili linagamula kuti mlongoyu azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake kwa zaka ziwiri ndi hafu. Panopa sakuyenera kupita kundende.