Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Yevgeniy Yegorov

APRIL 1, 2021
RUSSIA

Khoti la ku Russia Linaphwanya Ufulu Wolambira wa M’bale Yevgeniy Yegorov

Khoti la ku Russia Linaphwanya Ufulu Wolambira wa M’bale Yevgeniy Yegorov

Chigamulo

Khoti la m’Boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda, posachedwapa lipereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Yevgeniy Yegorov. * Loya woimira boma pa mlanduwu akuyembekezeka kupempha kuti m’baleyu akakhale kundende.

Zokhudza M’baleyu

Yevgeniy Yegorov

  • Chaka chobadwa: 1991 (ku Birobidzhan)

  • Mbiri yake: Analeredwa ndi amayi komanso agogo ake. Iye anaphunzira ntchito yamagetsi ndipo amagwira ntchito yokonza maloko. Amakonda kuwerenga ndi kulemba ndipo analemba buku komanso ndakatulo zambiri. Mu 2005, anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Mu September 2019 anakwatirana ndi Kseniya ndipo anakhala ndi mwana wamwamuna mu August 2020.

Mlandu Wake

Mu May 2018, apolisi a gulu la chitetezo (FSB) anakachita chipikisheni m’nyumba za anthu ambiri ku Birobidzhan. Kutangotsala nthawi yochepa kuti apange ukwati, Yevgeniy anaimbidwa mlandu chifukwa cha zimene amakhulupirira komanso chifukwa chowerenga Baibulo. Iye analetsedwa kuyenda maulendo osiyanasiyana. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene ukwati wa Yevgeniy unachitika, nawonso mayi ake a Larisa Artamonova, anaimbidwa mlandu. Mlandu wa Yevgeniy unayamba kuzengedwa mu December 2019, ku khothi la mumzinda wa Birobidzhan.

Yevgeniy ananena kuti panopa amaona kuti ali pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova. Iye anati: “Pa nthawi yovuta kwambiri imeneyi Yehova anandithandiza kukhazika mtima pansi ndiponso anandipatsa ‘mphamvu yoposa yachibadwa.’”—2 Akorinto 4:7.

Ngakhale kuti Yehova akumuthandiza, Yevgeniy akudziwa kuti ayenera kukonzekera zinthu zimene angadzakumane nazo m’tsogolo. Iye anafotokoza kuti: “Chinthu chofunika kwambiri kwa ine, ndi kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova mosasamala kanthu kuti zinthu zili bwanji pa moyo wanga.”

Ngakhale kuti akuzunzidwa, ndife otsimikizira kuti Yevgeniy ndi Kseniya, komanso abale ndi alongo onse a ku Russia, alimbikitsidwa kwambiri ndi mawu ouziridwa a pa Salimo 10:17 omwe amati: “Mudzamva kuchonderera kwa anthu ofatsa, inu Yehova. Mudzakonzekeretsa mitima yawo. Mudzatchera khutu lanu.”

^ N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo