Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Kirill Yevstigneev

13 JANUARY, 2022
RUSSIA

Kudalira Yehova Kwathandiza M’bale Yevstigneev Kuti Apitirize Kukhala Wokhulupirika

Kudalira Yehova Kwathandiza M’bale Yevstigneev Kuti Apitirize Kukhala Wokhulupirika

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. Khoti la mu mzinda wa Nizhny Novgorod, m’boma la Leninskiy, posachedwa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Kirill Yevstigneev. Loya wa boma sananene chilango chimene akufuna kuti M’bale Yevstigneev apatsidwe

  2. 8 October, 2021

    Mlandu unayamba kuweruzidwa. Polankhula ndi a jaji, a Yevstigneev anafotokoza kuti sankachititsa msonkhano wachipembedzo, koma kuti anthu anangosonkhana kuti achite phwando

  3. 24 August, 2021

    Apolisi analetsa M’bale Yevstigneev kuti asamayendeyende

  4. 2 September, 2020

    A Yevstigneev anawatsegulira mlandu woti “ankapereka ndalama zoyendetsera gulu lochita zinthu zoopsa” chifukwa choti anachita lendi chipinda chochitiramo msonkhano

  5. 11 July, 2019

    Apolisi anayamba kufufuza za M’bale Yevstigneev chifukwa choti ndi amene anasainira zikalata zoti adzagwiritsa ntchito chipinda chochitiramo msonkhano. Choncho apolisi anakafufuza zinthu kunyumba kwawo

  6. 4 June, 2019

    Apolisi anatsegula mlandu koma “sanatchule dzina la munthu” amene ankamufufuzayo. Anatsegula mlanduwo chifukwa choti anthu anachita msonkhano

  7. April 2019

    M’bale Yevstigneev ndi a Mboni za Yehova angapo ku Nizhny Novgorod, anachita lendi chipinda kuti achitiremo phwando

Zokhudza M’baleyu

Chikhulupiriro chathu chimalimba tikamva za kulimba mtima komwe M’bale Yevstigneev, mkazi wake komanso abale ndi alongo onse okhulupirika a ku Russia ndi ku Crimea akukusonyeza, ngakhale kuti akuzunzidwa. Afilipi 1:13, 14.