Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumanzere kupita: M’bale Aram Danielyan, Denis Kuzyanin, Sergey Polosenko, ndi Nikolay Vasiliyev

14 DECEMBER 2023
RUSSIA

“Kukhulupirira Yehova Kwandithandiza Kwambiri”

“Kukhulupirira Yehova Kwandithandiza Kwambiri”

Posachedwapa, khoti la m’boma la Samarskiy lilengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza abale otsatirawa: Aram Danielyan, Denis Kuzyanin, Sergey Polosenko, ndi Nikolay Vasiliyev. Loya woimira boma pamlanduwu akuyembekezeredwa kusankha chigamulo chimene akufuna kuti abalewa apatsidwe.

Zokhudza Abalewa

Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kutonthoza atumiki ake onse amene akukumana ndi mavuto chifukwa cha chikhulupiriro chawo ndipo iye ‘awalimbikitsa kuti nthawi zonse azichita komanso kulankhula zinthu zabwino.’​—2 Atesalonika 2:16, 17.

Nthawi ndi Zochitika

  1. 14 December 2021

    Denis, Nikolay, ndi Sergey anaganiziridwa kuti apalamula mlandu

  2. 15 December 2021

    Apolisi anafufuza m’nyumba ya Nokolay ndi Sergey. Kenako abalewa anamangidwa ndi kukasungidwa kundende yongoyembekezera

  3. 16 December 2021

    Denis, Nikolay, ndi Sergey anasamutsidwa n’kupita nawo kundende yomwe anthu amakhala poyembekezera kuzengedwa mlandu

  4. 6 January 2022

    Aram anaganiziridwa kuti wapalamula mlandu ndipo anamumanga ali kubwalo la ndege

  5. 7 January 2022

    Aram anaikidwa m’ndende yomwe anthu amakhala poyembekezera kuwazenga mlandu

  6. 12-14 December 2022

    Abale onse 4 anatulutsidwa m’ndende ndipo analetsedwa kuchita zinthu zina

  7. 16 June 2023

    Khoti linayamba kuwazenga mlandu