Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Aleksandr Kabanov

8 AUGUST, 2022
RUSSIA

Kukonzekera Kunathandiza M’bale Aleksandr Kabanov Kukhala Wodekha

Kukonzekera Kunathandiza M’bale Aleksandr Kabanov Kukhala Wodekha

Posachedwa Khoti la Krasnoyarsk lomwe lili m’Chigawo cha Zelenogorsk lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Aleksandr Kabanov. Loya woyimira boma wapempha kuti khoti lipatse m’baleyu chilango chokakhala kundende zaka ziwiri ndi hafu.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 26 December, 2019

    M’bale Kabanov anamangidwa chifukwa chochita nawo zinthu za gulu lomwe linaletsedwa ndi boma poliganizira kuti limachita zinthu zoopsa. Komanso chifukwa chakuti ankawerenga Baibulo ndi kuuza ena zokhudza Yehova. Anaikidwa m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu

  2. 27 December, 2019

    Anatulutsidwa m’ndende, jaji atakana zomwe loya waboma anapempha kuti m’baleyu akakhale m’ndende poyembekezera kuzengedwa kwa mlandu wake

  3. 6 December, 2021

    M’bale Kabanov anayankhula mawu ake omaliza mu khoti. M’malo mopereka chigamulo, jaji analamula kuti nkhaniyo ikafufuzidwenso bwino, zomwe zinachititsa kuti mlanduwu uimitsidwe kaye kwa kanthawi

  4. 25 March, 2022

    Mlandu unayambiranso kuzengedwa

Zokhudza M’baleyu

Abale ndi alongo athu ku Russia ndi zitsanzo pa nkhani yosonyeza chikhulupiriro chifukwa amatsatira mawu opezeka pa Yesaya 12:2 akuti: “Taonani! Mulungu ndiye chipulumutso changa. Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse, pakuti Ya Yehova ndiye mphamvu zanga ndi nyonga zanga.”