Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuyambira kumanzere kupita kumanja: M’bale Anton Chermnykh, Sergey Korolchuk, ndi Dmitriy Tishchenko

JULY 14, 2021
RUSSIA

Kukonzekereratu Chizunzo Kunathandiza Abale Atatu Kukhalabe Okhulupirika kwa Yehova

Kukonzekereratu Chizunzo Kunathandiza Abale Atatu Kukhalabe Okhulupirika kwa Yehova

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. Khoti la m’Boma la Ussuriyskiy m’Chigawo cha Primorye posachedwapa lilengeza chigamulo chake pa mlandu wa abale awa: Anton Chermnykh, Sergey Korolchuk ndi Dmitriy Tishchenko. * Loya woimira boma pa mlandu akuyembekezeka kupempha kuti abalewa akakhale kundende

  2. 23 September 2020

    A khoti anayamba kumvetsera mlandu wa Anton, Sergey ndi Dmitriy

  3. 7 July 2020

    Abalewa, Anton, Sergey ndi Dmitriy akuwazenga mlandu woti ndi atsogoleri a gulu la chipembedzo lomwe ndi loletsedwa chifukwa limachita zinthu zoopsa

  4. 18 June 2019

    M’bale Sergey anamutsekera m’ndende masiku awiri poyembekezera kumuzenga mlandu

Zokhudza Abalewa

Pamene mlandu wawo ukupitirira, tikudziwa kuti Yehova adalitsa kukhulupirika kwa Anton, Sergey, ndi Dmitriy.—Miyambo 28:20.

^ N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo