22 APRIL, 2021
RUSSIA
Kupemphera, Kuphunzira ndi Kulimbikitsana Zinathandiza Abale Kupirira Pamene Anatsekeredwa Komanso Kuuzidwa Kuti Asachoke Pakhomo
Tsiku la Mlandu
Posachedwapa khoti la m’boma la Pervomayskiy ku Kirov lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Maksim Khalturin, Vladimir Korobeynikov, Andrzej Oniszczuk, Andrey Suvorkov, Yevgeniy Suvorkov ndi Vladimir Vasilyev. a
M’bale Yuriy Geraskov, yemwe ankaimbidwanso mlanduwu anamwalira usanathe kuzengedwa.
Zokhudza Abalewa
Yuriy Geraskov
Kubadwa: 1956 (ku Azerbaijan)
Anamwalira: Pa 24 April 2020
Mbiri yake: Ali mnyamata ankakonda mpira ndi kujambula zithunzi. Ankagwira ntchito m’gulu lina lake la oimba. Anasamukira ku Russia mu 1993 chifukwa cha mavuto a zandale ku Azerbaijan. Mu 2011 anakwatira Alevtina ndipo m’chaka chomwechi anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Banjali linkakonda kuwongola miyendo kunja komanso kupita kukacheza kwa anzawo.
Maksim Khalturin
Kubadwa: 1974 (ku Kirov)
Mbiri yake: Ali mwana ankakonda kuwerenga. Anayamba kuphunzira Baibulo mu 1993. Anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova mu 1995. Iye amasamalira makolo ake okalamba. Makolo akewa ndi achipembedzo china koma amalemekeza zimene iye amakhulupirira
Vladimir Korobeynikov
Kubadwa: 1952 (pachilumba cha Dikson m’chigawo cha Krasnoyarsk)
Mbiri yake: Bambo ake anali asayansi yoona za nyanja kumpoto kwenikweni kwa dziko. Ali mwana Vladimir ankakonda kupanga zinthu zosiyanasiyana. Kenako anayamba ntchito ya upulambala komanso yokonza makina osiyanasiyana. Panopa anapuma pantchito ndipo amakonda kupha nsomba
Iye ndi mkazi wake dzina lake Olga, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova cha mu 1990 ndipo ankachita chidwi kwambiri maulosi a m’Baibulo. Anabatizidwa mu 1996. Ali ndi mwana wamwamuna wamkulu komanso wamkazi ndipo mfundo za m’Baibulo zathandiza banja lawo lonse kukhala losangalala.
Andrzej Oniszczuk
Kubadwa: 1968 (ku Białystok m’dziko la Poland)
Mbiri yake: Ali mnyamata ankakonda kusewera mpira komanso kunyamula zitsulo. Anabatizidwa mu 1990 ndipo anasamukira ku Kirov mu 1997. Iye amakonda mabuku a Chirasha. Mu 2002 anakwatira Anna. Iwo amakonda kukhala panja, kuzula bowa komanso kusewera mpira.
Andrey Suvorkov
Kubadwa: 1993 (Ku Kirov)
Mbiri yake: Mayi ake anamuphunzitsa choonadi kuyambira ali mwana. Ali mwana ankakonda kuphunzira sayansi, komanso kuchita masewera osiyanasiyana. Mu 2007 anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Atakana usilikali ankagwira ntchito m’chipatala chothandiza anthu ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Mu 2016 anakwatira Svetlana. Onse amakonda kuchita masewera osiyanasiyana
Yevgeniy Suvorkov
Kubadwa: 1978 (ku Kirov)
Mbiri yake: Ali mwana ankakonda kusewera osiyanasiyana komanso kumvetsera nyimbo. Iye amagwira ntchito zamagetsi. Anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ali ndi zaka 16. Anabatizidwa mu 1995. Ali ndi zaka 18 anakana usilikali n’kupempha ntchito ina. Anapatsidwa ntchito inayo pambuyo poimbidwa mlandu maulendo 6. Mu 2000 anakwatira Svetlana ndipo anathandizana naye kulera mwana wake dzina lake Andrey (yemwe tamutchula pamwambapa)
Vladimir Vasilyev
Kubadwa: 1956 (ku Perm)
Mbiri yake: Ali mwana ankakonda kusewera mpira. Ankagwira ntchito ya upulambala ndi yoyendetsa galimoto. Panopa anapuma pa ntchito. Iye ndi mkazi wake Nadezhda anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova cha mu 1990 ndipo anabatizidwa mu 1994
Mlandu Wawo
Pa 9 October, 2018, apolisi anachita chipikisheni m’nyumba 14 za a Mboni za Yehova ku Kirov. Pa nthawiyi, M’bale Brothers Maksim Khalturin, Vladimir Korobeynikov, Andrzej Oniszczuk, Andrey Suvorkov, ndi Yevgeniy Suvorkov anatsekeredwa. Kenako anakaikidwa kumalo ena potidikira mlandu wawo. Ndiyeno mu January 2019, M’bale Vladimir Vasilyev anayamba kuimbidwa mlandu ndipo mu July, M’bale Yuriy Geraskov anayambaso kuimbidwa mlanduwu.
Vladimir Korobeynikov anatsekeredwanso kwa miyezi yoposa iwiri. Iye anamasulidwa kuti azikasamalira mkazi wake yemwe akudwala komanso mwana wake. Koma anauzidwa kuti asamachoke pakhomo. Maksim ndi Andrey anatsekeredwa kwa nthawi yoposa miyezi itatu podikira mlandu wawo. Yevgeniy anatsekeredwa pafupifupi kwa miyezi 5. Andrzej anatsekeredwa kwa masiku 327. Pa gulu la abalewa, ena anatulutsidwa koma anauzidwa kuti asamachoke pakhomo. Panopa anamasulidwa koma anauzidwabe kuti asamachoke m’dera lawo.
Pa nthawi imene anatsekeredwayi, abalewa anawasiyanitsa ndi mabanja awo ndipo zimene zinalizopweteka kwambiri. Koma iwo sankakayikira kuti Yehova adzasamalira mabanjawo.
Mwachitsanzo, Olga, yemwe ndi mkazi wa Vladimir Korobeyniko, ndi wolumala. M’baleyu anati: “Zinkandiwawa kwambiri kuti mkazi wanga yemwe amafunika kumuthandiza ndamusiya yekha kunyumba.” Iye ananenanso kuti, apolisi analanda foni ya mkazi wangayo pa nthawi ya chipikisheni. Zimenezi zinkamudetsa nkhawa kwambiri Vladimir mpaka pamene analandira kalata yochokera kwa alongo ena amene anamuuza kuti Akhristu anzake akusamalira mkazi wake. Kenako analandiranso kalata yolimbikitsa yochokera kwa Olga yomutsimikizira kuti ali bwinobwino.
Kuuzidwa kuti usachoke pakhomo komanso kuimbidwa mlandu wochita zinthu zoopsa kumabweretsa mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, n’zovuta kuti abale apeze ntchito zodalirika. Anatsekeredwanso ma akaunti awo a kubanki.
Koma Yevgeniya anati: “Yehova amapereka mowolowa manja zinthu zofunika pa moyo wathu. Mofanana ndi Aisiraeli m’chipululu, sitisowa kanthu. Taona banja la Yehova likutithandiza potipatsa zinthu kutilimbikitsa komanso kutisamalira mwauzimu.
Abalewa amanena kuti kupemphera, kuphunzira paokha komanso kuwerenga Baibulo kwawathandiza kuti akhale olimba mtima komanso asafooke. Mwachitsanzo, Vladimir Vasilyev ananena kuti: “Nkhani za m’Baibulo zatithandiza kuzindikira kuti Yehova ndi wamphamvu ndipo amaona zonse zimene zikuchitika. Panopa timakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse komanso kumudalira kwambiri kuposa kale.”
N’zoona kuti milanduyi yabweretsa mavuto ambiri kwa abale athuwa ndi mabanja awo. Koma sitikukayikira kuti apitiriza kudalira Yehova. Apitirizanso kupirira pokumbukira kuti mavuto amene “munthu” angawabweretsere ndi akanthawi.—Salimo 56:4.
a Nthawi zina sizitheka kudziwiratu tsiku lopereka chigamulo.