Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Anatoliy Gorbunov ndi mkazi wake Galina

AUGUST 5, 2021
RUSSIA

Kupemphera Mosalekeza Kwathandiza M’bale Anatoliy Gorbunov Kukhalabe Wosangalala

Kupemphera Mosalekeza Kwathandiza M’bale Anatoliy Gorbunov Kukhalabe Wosangalala

Nthawi ndi Zochitika

  1. Khoti la m’Boma la Oktyabr’skiy lomwe lili m’Chigawo cha Krasnoyarsk, lipereka chigamulo chake posachedwapa pa mlandu wa M’bale Anatoliy Gorbunov a

  2. Pa 9 February 2021

    Mlandu wa M’bale Anatoliy unayamba kuzengedwa

  3. Pa 15 September 2020

    Akuluakulu a boma anachita chipikisheni nyumba ya m’baleyu ndipo anatenga makiyi a nyumba yake

  4. Pa 25 March 2020

    M’bale Anatoliy anam’tsegulira mlandu. Ankamuimba mlandu wotsogolera misonkhano ya chipembedzo ya gulu lomwe ndi loletsedwa

  5. Pa 7 November 2018

    Akuluakulu a boma anachita chipikisheni nyumba ya M’bale Anatoliy m’mawa kwambiri. Iwo anatenga laputopu, tabuleti, fulashi, chipangizo china chosungiramo zinthu pa kompyuta, komanso mafoni awiri. M’baleyu anamutengera ku maofesi a komiti yofufuza milandu ya dziko la Russia komwe anakamufunsa mafunso ndipo anamumasula patadutsa ola limodzi.

Zokhudza M’baleyu

Pamene M’bale Anatoliy ndi banja lake akupitirizabe kudalira Yehova mwa kupemphera kwa iye, tikukhulupirira kuti iye awathandiza kuti apitirizebe kukhala osangalala.—Salimo 25:1, 2.

a Tsiku lenileni lopereka chigamulo nthawi zina silimadziwikiratu.