Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Anton Ostapenko

28 APRIL 28, 2021
RUSSIA

Kupemphera ndi Kuimba Nyimbo za Ufumu Kunathandiza M’bale Anton Ostapenko Pamene Anatsekeredwa

Kupemphera ndi Kuimba Nyimbo za Ufumu Kunathandiza M’bale Anton Ostapenko Pamene Anatsekeredwa

Tsiku Lopereka Chigamulo

Posachedwapa, khoti la mumzinda wa Sharypovo m’chigawo cha Krasnoyarsk lipereka chigamulo pa mlandu wa Mbale Anton Ostapenko. *

Zokhudza M’baleyu

Anton Ostapenko

  • Kubadwa: Mu 1991 (Ku Ekibastuz m’dziko Kazakhstan)

  • Mbiri yake: Amagwira ntchito yoona kuti pamalo opangira magetsi ndi otetezeka. Iye ndi mchewali wake ali achinyamata, mayi awo anayamba kuwaphunzitsa Baibulo. Iye anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova mu 2005

    Mu 2015, iye anakwatira Natalya ndipo amakonda kusewera pa sinowo ndi ayisi. Anton amakondanso kuimba gitala, kuwedza nsomba ndi kusewera tenisi

Mlandu Wake

Pa 19 April 2019, apolisi ku Sharypovo anachita chipikisheni m’nyumba 10 za a Mboni za Yehova n’kumafunsa mafunso abale ndi alongo amene anawapeza. M’bale Anton Ostapenko anamangidwa n’kukatsekeredwa podikira mlandu wake ndipo anamasulidwa pa 20 December, 2019. Iye akuimbidwa mlandu wotsogolera pa zinthu zokhudza gulu loopsa.

Pa miyezi 6 imene Anton anatsekeredwa nthawi zina ankachoka pamene pali kamera n’kupita pasinki muselo yake kukalira chifukwa chopwetekedwa mtima.

Akapemphera m’pamene ankapeza mphamvu. Anton anati: “Ndinachonderera Yehova kuti andithandize kupirira.” Iye ananenanso kuti: “Pali zinthu zambiri zimene ndinaphunzira. Kumeneku ndinakula mwauzimu n’kukhala munthu wamphamvu. . . . N’zochititsa chidwi kuti munthu ukakumana ndi mavuto ngati amenewa zimakhala wachoka m’kalasi kupita kumalo oti ugwiritse ntchito zimene unaphunzirazo. Ndipo si nthawi zonse pamene umakhala ndi Baibulo muselo. Choncho ndisanapite kundende ndinkangowerenga za Yehova. Koma ndili kundendeko, Yehova anandisonyeza makhalidwe ake. Kunena zoona zimenezi zinandisangalatsa kwambiri. Ndinaphunzira kuti sikuti wangokhala Mulungu Wamphamvuyonse koma ndi Atate wachikondi amene amamvetsa mavuto athu n’kutithandiza pa nthawi yoyenera m’njira imene sitinkaiganizira.”

Nyimbo za Ufumu zinkamulimbikitsanso kwambiri. “Ine ndi mkazi wanga tinkakonda kuimba limodzi nyimbo ndipo izi zinandithandiza kuti ndiziloweze. Atanditsekera ndinkazikumbukira nyimbo zimenezi moti magetsi akazima ndinkapemphera komanso kuimba nyimbo ndipo izi zinkandithandiza kuti ndizigona mtima uli m’malo.”

Panopa Anton akudikira chigamulo cha mlandu wake uku akugwira ntchito yake. Koma anauzidwa kuti asadzatuluke mumzinda wa Sharypovo. Zimenezi zimachititsa kuti azilephera kuperekeza mayi ake kuchipatala.

Timapemphera nthawi zonse kuti Yehova apitirize kupereka mtendere wake kwa abale athu amene akuzunzidwa.—Yohane 14:27.

^ Nthawi zina tsiku lenileni lopereka chigamulo silidziwika