Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 1, 2018
RUSSIA

Khoti la ku Oryol Lidzapitiriza Kumvetsera Mlandu wa Dennis Christensen pa 3 April 2018

Khoti la ku Oryol Lidzapitiriza Kumvetsera Mlandu wa Dennis Christensen pa 3 April 2018

Pa 26 February 2018, mlandu wa a Dennis Christensen unayamba kuzengedwa kukhoti la ku Oryol. Anthu ambiri amene ali kumbali ya a Christensen anali kukhotilo. Kunalinso munthu wina woimira boma la Denmark dzina lake Jeanne Christina Demirci, yemwe amagwira ntchito ku ofesi ya kazembe ku Moscow. Patangopita ola limodzi lokha, Woweruza Aleksey Rudnev anavomera pempho la loya wa a Christensen kuti akhale ndi nthawi yowonjezera yoti awerenge nkhani zonse zokhudza mlanduwu. Mlanduwu usanayambe kuzengedwa, khoti lina linali litapatsa loyayo milungu iwiri yokha kuti awerenge nkhanizo ngakhale kuti zinali zamasamba 2,500 ndipo zinalembedwa m’Chirasha. Woweruza Rudnev ananena kuti adzapitiriza kumvetsera mlanduwu pa 3 April 2018 nthawi ya 10:30 m’mawa. Koma a Christensen akuwasungabe kundende podikira tsiku limenelo.