Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Aleksandr Lubin ndi mkazi wake, Tatyana

5 FEBRUARY 2024
RUSSIA

“Lola Kuti Yehova Akutsogolere Panjira Yako”

“Lola Kuti Yehova Akutsogolere Panjira Yako”

Posachedwapa, khoti la m’boma la Shadrinskiy m’chigawo cha Kurgan, lilengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Aleksandr Lubin. Loya woimira boma pa mlanduwu akuyembekezereka kunena chilango chimene akufuna kuti m’baleyu apatsidwe.

Zokhudza M’baleyu

Sitikukayikira kuti tonsefe tingakwanitse kupirira mokhulupirika mavuto aliwonse amene tingakumane nawo ngati tingadalire Yehova mofanana ndi M’bale Aleksandr.​—Yesaya 38:14.

Nthawi ndi Zochitika

  1. 13 July 2021

    Anamutsegulira mlandu

  2. 14 July 2021

    Nyumba 8 za a Mboni za Yehova zinafufuzidwa. M’bale Aleksandr anamangidwa, kufunsidwa mafunso komanso kutsekeredwa m’ndende poyembekezera mlandu wake

  3. 16 July 2021

    Anamusamutsira kundende ina poyembekezera kuzenga mlandu wake

  4. 19 July 2021

    Anachita apilo chifukwa choti ankadwala kwambiri

  5. 28 August 2021

    Pambuyo pomva pempho lochokera ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe komanso kwa anthu omenyera ufulu, Aleksandr anatulutsidwa m’ndende ndipo anapatsidwa chigamulo choti asamachoke m’dera limene amakhala

  6. 14 July 2023

    Khoti linayamba kuzenga mlandu

  7. 7 September 2023

    Khoti linaimitsa kaye kumvetsera mlanduwu chifukwa choti Aleksandr anagonekedwa m’chipatala