Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 30, 2020
RUSSIA

Loya Woimira Boma Wapanga Apilo N’cholinga Choti a Dennis Christensen Asatulutsidwe M’ndende Nthawi Yawo Isanakwane

Loya Woimira Boma Wapanga Apilo N’cholinga Choti a Dennis Christensen Asatulutsidwe M’ndende Nthawi Yawo Isanakwane

Tangodziwitsidwa posachedwapa kuti loya woimira boma dzina lake A. A. Shatunov, wa ku ofesi ya boma m’chigawo cha Kursk wapanga apilo yomwe ichititse kuti M’bale Dennis Christensen asatulutsidwe m’ndende nthawi yake isanakwane. Ngakhale kuti maloya ake akadandaula za nkhaniyi kukhoti, zitenga milungu ingapo kuti khoti lidzamvetsere mlanduwu. M’bale Christensen waikidwa muselo yozunzira anthu ndipo akhalamo masiku 10. Ngakhale kuti zinthu zasintha chonchi, komabe M’bale Christensen ali bwino. Zikomo kwambiri chifukwa chopitirizabe kupempherera M’bale ndi Mlongo Christensen.