JULY 1, 2020
RUSSIA
Loya Woimira Boma la Russia Waimitsa Chigamulo Choti M’bale Christensen Atulutsidwe
Pa 26 June 2020, oyang’anira ndende ya Lgov sanatsatire malamulo poika M’bale Dennis Christensen muselo yapadera yozunzira anthu yomwe amaikamo akaidi ophwanya malamulo a ndende. Zikuoneka kuti iwo achita zimenezi n’cholinga chomufooketsa popeza kuti thanzi lake lasintha ndipo silili bwino kwenikweni. Maloya a ku ofesi ya boma akumuneneranso milandu ina yabodza. Masiku apitawa, ofesiyi inapanga apilo kukhoti pogwiritsa ntchito milandu yabodza kuti M’bale Christensen asatulutsidwe nthawi yake isanakwane.
M’bale Christensen anagamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 6 ndipo pofika pano wakhala ali m’ndende kwa zaka zoposa zitatu. Panopa padutsa chaka chimodzi m’baleyu atakwanitsa zaka zimene akhoza kutulutsidwa m’ndende moti n’kupatsidwa chigamulo choti chigwirizane ndi nthawi yake yotsala. M’bale Christensen anapempha katatu kuti atulutsidwe koma anamukaniza. Atayesanso ulendo wina, khoti linavomera ndipo pa 23 June 2020, khoti la m’boma la Lgov linagamula kuti alipire chindapusa kuti chigwirizane ndi zaka zimene zatsala. Zitatero, loya woimira boma, a Artem Kofanov anagwirizana ndi chigamulochi.
Patadutsa masiku awiri, a Aleksei Shatunov omwe ndi loya wina woimira boma, anapempha khoti kuti lichotse chigamulochi ponena kuti ndi chosemphana ndi malamulo ndipo anapempha kuti mlanduwu uzengedwenso ndi woweruza wina. A Shatunov ananena izi potengera zimene zinali m’malipoti ena abodza ochokera kwa oyang’anira ndende ya Lgov. Malipotiwo ananena kuti M’bale Christensen alibe “mbiri yabwino pa nkhani yogwira ntchito komanso mmene amachitira zinthu kundendeko.”
Pamene khoti linkamvetsera mlandu wa M’bale Christensen pa 23 June, oyang’anira ndende anayesa kupereka malipoti omwewo koma woweruza milandu anagamula kuti zimene ankanenazo zinali zosamveka. Loya woimira a Christensen anasonyeza umboni wachipatala m’khoti wotsimikizira zoti M’bale Christensen sakanakwanitsa kugwira ntchito yolemetsa mundendeyo chifukwa choti thanzi lake silili bwino. Pofotokoza mbali yake, woimira ndende anavomereza kuti potengera ndi mmene thanzi la M’bale Christensen lilili, sakanatha kuwapatsa ntchito iliyonse yoti agwire.
Pa nthawi imene maloya a kuofesi ya boma ankayendetsa zokhudza apilo n’cholinga choti M’bale Christensen asatulutsidwe m’ndende, oyang’anira ndende anatumiza kukhoti malipoti awiri okhudza M’bale Christensen. Lipoti loyamba linanena kuti anamupeza m’chipinda chodyera pa nthawi yolakwika, pamene lipoti lachiwiri linati analowa m’nyumba ya asilikali atavala tisheti popanda kuvala jekete. Chifukwa cha zimenezi, oyang’anira ndende anaika M’bale Christensen muselo yozunzira anthu kwa masiku 10. Malamulo a dziko la Russia amanena kuti akuluakulu a ndende amayenera kuchita zimenezi pokhapokha ngati mkaidi waphwanya malamulo a ndende mobwerezabwereza ndipo m’kaidiyo amafunika kuyezedwa kaye ndi dokotala kuti aone mmene thanzi lake lilili asanaikidwe muselo imeneyo. Choncho popeza kuti M’bale Christensen sanapalamule mlandu woterowo komanso sanayezedwe ndi dokotala, zinali zosayenera kuti aikidwe muselo imeneyo.
Pakali pano M’bale Christensen ali muselo yaing’ono mamita atatu mulitali ndi mamita awiri mulifupi ndipo akukhala limodzi ndi mkaidi wina. M’chipindachi muli nkhungu ndiponso mulibe mpweya wokwanira ndipo zimenezi zikhudza thanzi la M’bale Christensen lomwe ndi lofooka kale. Miyezi yapitayi anadwala chibayo komanso anamupeza ndi matenda oopsa a msana. Loya wa M’bale Christensen ananena kuti “ngakhale kuti akuluakulu a ndende akudziwa zimenezi, anaika m’baleyu muselo yomwe akumagona pabedi lolimba ndipo akumamva kupweteka kwambiri.”
M’bale Christensen anauza loya wake kuti pa nthawi imene ankaganiziridwa kuti anaphwanya malamulo a ndende analinso limodzi ndi akaidi ena koma enawo sanaikidwe muselo yozunzira anthu. Loya wa M’bale Christensen ananena kuti: “Zimenezi zikutichititsa kukhulupirira kuti akuluakuluwa anachitira dala kuti cholinga chawo choti zimene khoti linagamula kuti M’bale Christensen atulutsidwe m’ndende zisatheke.”
Pamene akuluakulu a boma la Russia akupitirizabe kukonza njira zatsopano komanso kuchitira nkhanza abale athu ku Russia, sitisiya kukhulupirira kuti Yehova akhala malo awo achitetezo. Tiyeni tipitirize kupemphera kuti Yehova athandize M’bale Christensen ndi mkazi wake Irina kuti akhalebe okhulupirika pa nthawi yovuta kwambiri imeneyi.—Salimo 94:13, 21, 22.