Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Dennis Christensen akuperekezedwa ku khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy ku Oryol

JULY 31, 2019
RUSSIA

MMENE ZINTHU ZILILI PANOPA—A Dennis Christensen Adakali Okhulupirika Atawasamutsira Kundende Ina

MMENE ZINTHU ZILILI PANOPA—A Dennis Christensen Adakali Okhulupirika Atawasamutsira Kundende Ina

Pa 6 June, 2019, patatha milungu iwiri M’bale Dennis Christensen ataluza apilo ya mlandu wake, akuluakulu a boma la Russia anamusamutsa muselo yomwe anaikidwa poyembekezera kuzengedwa mlandu ya mumzinda wa Oryol ndipo anamupititsa kundende yotchedwa Penal Colony No. 3 mumzinda wa Lgov. Mzinda wa Lgov uli pamtunda wa makilomita pafupifupi 200 kuchokera ku Oryol, komwe banja la a Christensen komanso anzawo amakhala.

A Christensen atangofika kumene kundendeyi, ananyozedwa komanso anthu ena anayesetsa kuwachititsa kuti asiye kukhala okhulupirika. Ngakhale kuti anachitidwa zimenezi, a Christensen akhala akudalira kwambiri Yehova ndipo zimenezi zawathandiza kukhala olimba komanso opanda mantha.—1 Petulo 5:10.

Ku Finland (kuchokera kumanzere kupita kumanja): M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira, Irina Christensen, ndi Tommi Kauko wochokera ku Finland

Kungoyambira pamene M’bale Christensen anamangidwa n’kuikidwa m’ndende, abale ayesetsa kuthandiza komanso kusamalira mkazi wake Irina. M’mwezi wa June, M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira komanso abale ena audindo anapita kukakumana ndi Irina m’dziko la Finland kuti akamulimbikitse.

M’bale Christensen wakhala ali m’ndende yatsopanoyi yomwe ili kutali kwambiri ndi kwawo, kwa mwezi woposa umodzi tsopano. Posachedwapa, Irina anapatsidwa chilolezo kuti azilankhulana ndi mwamuna wake kamodzi patsiku kudzera pa telefoni. Analoledwanso kuti azipita kundendeyo kukamuona.

Irina akuwerenganso makalata olimbikitsa ochokera kwa a Dennis Christensen

Ngakhale kuti M’bale Christensen komanso Irina akumana ndi mavuto osiyanasiyana kwa zaka ziwiri zapitazi kuchokera pamene m’baleyu anamangidwa n’kuikidwa m’ndende, iwo akadali okhulupirika komanso achimwemwe. Irina ananena kuti makalata omwe amalandira kuchokera kwa M’bale Christensen mlungu uliwonse akhala akumulimbikitsa kwambiri. M’kalata ina yomwe Irina amaikonda kwambiri, M’bale Christensen analemba kuti: “Kukhala ndi maganizo oti zinthu zikhala bwino n’kumene kumathandiza kuti munthu apambane ndipo tili ndi zifukwa zambiri zokhalira achimwemwe.” M’kalatayi, iye anamaliza kuti: “Cholinga chomwe tilili ndi moyo n’choti tizisonyeza kuti tili kumbali ya Yehova monga woyenera kulamulira. Ndikudziwa kuti ulendo wathuwu ndi wautali ndipo panopa sitinapambanebe. Koma pamapeto pake tipambana. Ndipo ndikukhulupirira ndi mtima wanga wonse kuti tipambana.”

Pa 21 July, kumsonkhano wamayiko womwe unachitikira ku Denmark, M’bale Lett wa m’Bungwe Lolamulira anawerenga uthenga wochokera kwa M’bale Christensen, womwe mbali yake ina unati: “Ndikanakonda ndikanasonkhana nanu, koma pa nthawi ino sizingatheke popeza sindinamalizebe utumiki womwe ndikuchita panopa. Koma zidzatheka m’tsogolomu, ndipo ndikuyembekezera mwachidwi kudzakhala nanu.”

Pamene anamangidwa ku Rome, Paulo analemba kuti: “Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira za inu. Ndimachita zimenezi m’pembedzero langa lililonse limene ndimapereka mosangalala chifukwa cha nonsenu.  . .  inu ndinu apamtima panga, ndiponso nonsenu ndinu ogawana nane m’kukoma mtima kwakukulu, m’maunyolo anga m’ndende, ndi pa kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.”—Afilipi 1:3, 4, 7.