MAY 1, 2020
RUSSIA
Mayiko a ku Europe Adzudzula Boma la Russia Chifukwa Chozunza a Mboni za Yehova
Pa 12 March 2020, nthumwi za mayiko oposa 30 a ku Europe zinadzudzula boma la Russia chifukwa chozunza abale athu. Zimenezi zinachitika pamsonkhano womwe bungwe la OSCE linachititsa Bungweli limatchedwa Organization for Security and Co-operation in Europe (OSCE) Permanent Council. Chimodzi mwa zolinga za bungwe la OSCE ndi kuteteza ufulu wachibadwidwe wa anthu padziko lonse.
M’chikalata chomwe chinawerengedwa pamsonkhanowu, mayiko 27 omwe ali mu Mgwirizano wa Mayiko a ku Europe (EU) komanso mayiko ena 6 omwe sali mumgwirizanowu, analengeza kuti, “Boma la Russia likumazunza a Mboni za Yehova. Apolisi akumapita kunyumba zawo n’kumakawagwira, kuwamanga popanda kuwauza chimene alakwa, kuwafufuza ngati zigawenga komanso kuwatsekera m’ndende popanda kuwazenga mlandu moti pofika pano ena akhala m’ndende kwa zaka 7. Bungwe la Mgwirizano wa Mayiko a ku Europe likuda nkhawa kwambiri ndi zimenezi. Komanso, takhumudwa kwambiri ndi malipoti omwe tamva akuti asilikali akundende akumazunza kwambiri a Mboni za Yehova komanso akuti apolisi akumawachitira nkhanza akamawasunga poyembekezera kuti awatumize kundende.”
Kazembe wa dziko la United Kingdom, dzina lake Neil Bush, ananenanso zotsatirazi: “Mu July 2017, khoti lalikulu la ku Russia linagwirizana ndi chigamulo chomwe khoti laling’ono linapereka. Chigamulochi chinkanena kuti a Mboni za Yehova ndi ‘kagulu koopsa.’ Zimenezi zinachititsa kuti a Mboni okwana 175,000 omwe ankalambira mwamtendere m’dzikoli akhale kagulu kosavomerezeka. Komanso khotili silinalemekeze ufulu wachipembedzo womwe umapezeka m’malamulo a dzikoli komanso m’zikalata zingapo zomwe dzikoli linavomereza pamaso pa bungwe la OSCE kuti liziwatsatira.” Kazembeyo anawonjezeranso kuti: “Kungochokera pamene khotili linagamula zimenezi, takhala tikuona a Mboni za Yehova ambiri akumangidwa, kufufuzidwa, komanso kuzengedwa milandu yosiyanasiyana ndi boma la Russia. Mofanana ndi zimene zanenedwa kale m’chikalata chija, nafenso tikuda nkhawa ndi zimene bomali likuchita pozunza a Mboni za Yehova.”
Nkhani ina imene inatchulidwa ndi nthumwi za mayiko a ku Europe ndi yokhudza kumenyedwa kwa a Mboni 5 pa 6 February 2020. Asilikali oyang’anira akaidi kundende ina (yotchedwa Penal Colony No. 1) anamenya M’bale Aleksey Budenchuk, Gennadiy German, Roman Gridasov, Feliks Makhammadiyev komanso M’bale Aleksey Miretskiy. Nthumwi yoimira bungwe la EU inati: “Anthu omwe anamenyedwawa anavulazidwa ndipo mmodzi [Feliks Makhammadiyev] anavulala kwambiri moti ankafunika kugonekedwa kuchipatala. Kuwonjezera pamenepa, pa 10 February 2020, Vadim Kutsenko anafotokoza kuti apolisi anamuzunza kwambiri asanamutumize kundende. Iye ananena kuti apolisiwo ankamumenya, kumukanyanga pakhosi komanso kumukhaulitsa ndi shoko pamene ankamukakamiza kuti aulule zinthu zokhudza a Mboni ena.”
Nthumwi yoimira bungwe la EU ija inakumbutsa anthu omwe anali pamsonkhanowo kuti: “Kuchitira nkhanza kapena kuzunza munthu ndi chimodzi mwa zinthu zoipa kwambiri zomwe zimaphwanya ufulu wachibadwidwe. Nkhanza zimachititsa munthu manyazi ndiponso kumuchotsera ulemu. Kuzunza munthu mwa njira imeneyi kukuphwanya malamulo omwe boma la Russia linavomera kuti liziwatsatira (boma la Russia linavomereza kuti lizilemekeza zigamulo zotsatirazi: Covenant on Civil and Political Rights, European Convention on Human Rights, komanso UN Convention against Torture and Other Cruel, Inhuman or Degrading Treatment or Punishment).”
Komanso, atsogoleri am’mayiko a ku Europe anatchulanso kuti zimene boma la Russia linkachitira a Mboni za Yehova ndi zosemphana ndi zimene bomali linalonjeza pamaso pa bungwe la OSCE zomwe zimasonyeza kuti abale ndi alongo athu m’dzikoli ali ndi ufulu wochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo.
Nthumwi yoimira bungwe la EU inanenanso kuti: “Pa 20 April 2017, khoti lalikulu ku Russia linalanda likulu la Mboni za Yehova komanso malo onse omwe ankawagwiritsa ntchito polambira ponena kuti gulu la Mboni za Yehova ndi ‘loopsa.’ Zimenezi zitachitika, takhala tikumva nthumwi yoimira dziko la Russia ikunena maulendo angapo pamsonkhano ngati uno kuti boma lawo lionetsetsa kuti a Mboni za Yehova akulambira mwaufulu. Akhalanso akutsindika mfundo yakuti m’dziko lawo muli ufulu wachipembedzo womwe umapatsa munthu mphamvu zosankha zimene akufuna kukhulupirira. Komabe tikupitirizabe kumva malipoti ambiri onena zoti apolisi akumagwira a Mboni m’nyumba zawo, akuwamanga mwachisawawa komanso kuti akumawafufuza ngati zigawenga.”
Atsogoleri a m’mayiko omwe ali m’bungwe la EU ananenanso kuti: “Kungochokera pamene a Mboni za Yehova analetsedwa kusonkhana ku Russia, apolisi akhala akupita kukagwira anthu kunyumba zawo zokwana 869, anthu okwana 26 ali kundende ndipo akudikirira kuti mlandu wawo uweruzidwe, 23 ali pa ukaidi wapanyumba, 316 anawatsegulira milandu ndipo 29 anapezeka kale kuti ndi olakwa.”
Kazembe Bush anati: “Ziwerengero zili pamwambazi zikusonyeza kuti a Mboni za Yehova akamachita zinthu zokhudza chipembedzo chawo, apolisi akumapita m’nyumba zawo n’kumakawagwira, akumawamanga kwa nthawi yaitali, akumawatsegulira milandu yosiyanasiyana kenako n’kuwatsekera m’ndende. Zimene apolisiwa akuchita pogwira a Mboni m’nyumba zawo, zikumachitika malo angapo m’tawuni imodzi komanso patsiku lofanana. Izi zikusonyeza kuti boma Russia lachita kukonza kuti lizizunza a Mboni za Yehova.”
Akatswiri oona za ufulu wachipembedzo anadzudzulanso zimene boma la Russia likuchitira abale athu. Pothirira ndemanga zimene nthumwi yoimira bungwe la EU linanena, Dr. Gudrun Kugler yemwe ndi loya wa ku Austria yemwenso ndi wandale komanso m’busa watchalitchi cha Katolika, anati: “Zinthu zikungoipiraipirabe ku Russia kungochokera pamene boma linaletsa ntchito yawo mu April 2017. . . . A Mboni za Yehova akumaimbidwa milandu chifukwa cha lamulo loletsa magulu omwe amachita zinthu monyanyira lomwe mabungwe omenyera maufulu a anthu akunena kuti ndi ‘losokoneza komanso losamveka bwinobwino.’ Apolisi akumagwiritsa ntchito lamulo limeneli (Gawo 282.2) pomanga anthu chifukwa choti ndi a Mboni za Yehova komanso chifukwa choti awapeza akuchita zinthu zokhudza chipembedzo chawo kunyumba kwawo. . . . Nkhanza zimenezi, zomwe boma la Russia likuchitira a Mboni za Yehova komanso magulu ena ang’onoang’ono a zipembedzo, ziyenera kutheratu!”
Nthumwi yoimira bungwe la EU inapitiriza kuti boma la Russia komanso mamembala a bungwe la OSCE “ali ndi udindo woonetsetsa kuti akuchita zonse zotheka kuti anthu asamazunzidwe. Akufunikanso kuonetsetsa kuti amene akuzunza anzawowo aziimbidwa mlandu, komanso kupereka chipukuta misozi kwa amene akuzunzidwawo.” Nthumwiyo inapitiriza kuti: “Choncho tikupempha boma la Russia kuti lichitepo kanthu mwamsanga pa malipoti onse okhudza nkhanza zimenezi. Aliyense amene akuchitira nkhanza mnzake alandire chilango choyenerera. . . . Tikupemphanso boma la Russia kuti lisiye kuzenga milandu komanso limasule anthu amene anamangidwa chifukwa chogwiritsa ntchito ufulu wawo wachipembedzo. Tikufunanso kupempha bomali kuti lisaiwale lonjezo lomwe linapanga pamaso pa mayiko ena kuti lidzalemekeza ufulu wachibadwidwe, ufulu wofotokoza maganizo ako, ufulu wochita zinthu ndi anthu ena, ufulu wosonkhana mwamtendere, ufulu wachipembedzo ndiponso ufulu wolowa m’magulu aang’ono komanso ufulu wozengedwa mlandu mwachilungamo.”
Kaya boma la Russia litsatira zimene mayikowa anapempha n’kuyamba kulemekeza ufulu wachipembedzo kapena ayi, tikudziwa kuti Yehova apitirizabe kuthandiza abale ndi alongo athu omwe ali kumeneko komanso kuwathandiza kuti apitirizabe kupirira mpaka pamene padzikoli padzakhale chilungamo chenicheni.—Salimo 10:18.