Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Aleksandr Bondarchuk ndi mkazi wake, Elena, (kumazere) ndi M’bale Sergey Yavushkin ndi mkazi wake, Tatiana (kumanja)

APRIL 2, 2021
RUSSIA

M’bale Aleksandr Bondarchuk ndi M’bale Sergey Yavushkin Posachedwa Alandira Chigamulo Atakhala Pa Ukaidi Wapanyumba Kwa Nthawi Yayitali

M’bale Aleksandr Bondarchuk ndi M’bale Sergey Yavushkin Posachedwa Alandira Chigamulo Atakhala Pa Ukaidi Wapanyumba Kwa Nthawi Yayitali

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la m’Boma la Zavodskoy ku Kemerovo posachedwapa lilengeza chigamulo chake pa mlandu wa m’bale Aleksandr Bondarchuk ndi m’bale Sergey Yavushkin. a

Zokhudza Abalewa

Aleksandr Bondarchuk

  • Chaka Chobadwa: 1974 (KuTopki, m’Chigawo cha Kemerovo)

  • Mbiri Yake: Bambo ake anamwalira iye ali ndi zaka 19. Anapita kusukulu kukaphunzira kugwiritsira ntchito makina akuluakulu komanso kuyendetsa magalimoto amene amagwiritsira ntchito pomanga, kenako anaphunzira ukalipentala. Panopa amagwira ntchito yokonza zinthu pa kampani ina. Amakonda kuwedza nsomba, kuchita masewera otsetsereka pa sinowo, kuyendetsa njira komanso kuthamanga

  • Anakwatirana ndi Elena mu chaka 1992. Mlongoyu anali munthu woyamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova m’banja lakwawo. Kugwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo kwathandiza kuti banja lawo likhale lolimba. Panopa ali ndi ana awiri amuna.

Sergey Yavushkin

  • Chaka Chobadwa: 1960 (Ku Rubtsovsk, m’Dera la Altai)

  • Mbiri Yake: Kwa zaka zambiri ankagwira ntchito ya zamagetsi komanso yowotcherera. Panopa amagwira ntchito yopanga maloko. Kuyambira ali wachinyamata amakonda kuimba gitala komanso kuchita masewera osiyanasiyana

  • Mu 1990 anakwatirana ndi Tatiana ndipo pasanapite nthawi yayitali anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Anagoma kwambiri kuona kuti ngakhale kuti Baibulo linalembedwa kalekale koma ndi buku lothandiza masiku ano. Ali ndi ana awiri, wamwamuna ndi wamkazi

Milandu Yawo

Pa 22 July, 2019, 6 sikisi koloko m’mawa, apolisi anachita chipikisheni kachiwiri kunyumba ya m’bale Aleksandr Bondarchuk ndi ya m’bale Sergey Yavushkin. Koma ulendo wachiwiriwu abalewa anawamanga ndipo akazi awo anawafunsa mafunso. Apolisiwo anawalandanso mafoni.

Abalewa anawatsekera kwa masiku awiri. Kenako Khoti la m’Boma la Kemerovo linawalamula kuti akhale pa ukaidi wapanyumba kwa miyezi iwiri koma kenako nthawiyi akhala akuiwonjezera kwa maulendo 6.

Pa ukaidi wapanyumbawu, abalewa sakuloledwa kuyenda mtunda wopitirira mamita 300 kuchokera pa nyumba zawo. Zimenezi zikutanthauza kuti sangapite kuntchito. Komabe abalewa asanayambe kuzengedwa milanduyi anali akudziwika kale m’dera lawo komanso kwa mabwana awo kuti ndi a khalidwe labwino. Chifukwa cha zimenezi, mabwana awowo anapempha wapolisi amene akutsogolera ntchito yofufuza milandu yawo kuti aziwalola kupita kuntchito. Koma wapolisiyo anakana pempho lawo.

M’bale Aleksandr ndi banja lake akhala akuona Yehova akuwathandiza mobwerezabwereza. Popeza kuti m’baleyu sakugwira ntchito panopa komanso ma akaunti awo akubanki anatsekedwa zikumakhala zovuta kuti azipeza ndalama. M’baleyu ananena kuti: “Mayesero amenewa ndikukumana nawowa andithandiza kuti ndizidalira komanso kukhulupirira kwambiri Yehova. Ndikuona kuti m’mbuyomu sindimatha kuona bwinobwino dzanja la Yehova likundithandiza. Koma panopa ndikuona kuti iye amandithandiza tsiku lililonse ndipo samandisiya ndekha ineyo kapena banja langa.”

M’bale Sergey amakhala ndi nkhawa kwambiri chifukwa cha mlandu wake. Zimenezi zachititsa kuti adwale matenda ofa ziwalo. Koma ngakhale akudwala sanataye mtima. Iye ananena kuti: “Mavuto akanthawi kochepa amene tikukumana nawo timafunika kumawaona ngati timavuto ting’onoting’ono ngakhale kuti nthawi zina zimakhala zovuta kupirira zimene zikutichitikira.”

Lemba la 1 Akorinto 15:58 ndi limene limathandiza m’Bale Sergey kukhala olimba. Lembali limanena kuti ‘zimene tikuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.’ M’baleyu ananena kuti: “Yehova amakumbukira chilichonse ndipo sadzaiwala ntchito zabwino zimene tikuchita.”

Tipitiriza kupempherera abale ndi alongo athu ku Russia amene kwa zaka zambiri akhala akupirira moleza mtima mayesero komanso kuzunzidwa. Apitirizebe kudalira komanso kupeza mphamvu m’Mawu a Mulungu omwe amati:: “Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa, amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.”—Salimo 147:11.

a N’zosatheka kudziwiratu tsiku limene khoti lidzapereka chigamulo chake.