Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuyambira kumanzere: M’bale Aleksandr Polozov ndi mkazi wake Svetlana; komanso M’bale Stepan Shevelev ndi mkazi wake Oksana

24 JANUARY, 2022
RUSSIA

M’bale Aleksandr Polozov ndi M’bale Stepan Shevelev Akudalitsidwa Ngakhale Akuzunzidwa

M’bale Aleksandr Polozov ndi M’bale Stepan Shevelev Akudalitsidwa Ngakhale Akuzunzidwa

Khoti la Mumzinda wa Norilsk m’Chigawo cha Krasnoyarsk, posachedwapa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Aleksandr Polozov komanso M’bale Stepan Shevelev. Loya woimira boma pa nkhaniyi sananene chilango chimene akufuna kuti abalewa apatsidwe.

Nthawi ndi Zochitika

  1. 20 October, 2019

    Apolisi anapita kumsasa wina mumzinda wa Norilsk ndipo a Mboni oposa 50 anamangidwa

  2. 26 October, 2019

    Aleksandr anamangidwa ndipo anaikidwa m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu

  3. 21 January, 2020

    Aleksandr anamasulidwa atakhala pafupifupi miyezi itatu m’ndende

  4. 19 February, 2020

    Aleksandr anaikidwa pa mndandanda wa anthu ochita zoopsa ndipo maakaunti ake a ku banki anatsekedwa

  5. 6 May, 2021

    Stepan ankaimbidwa mlandu “wolowa mu mgwirizano wochita zaupandu” ndi Aleksandr. Stepan ankaimbidwa “milandu” chifukwa chakuti ankapemphera komanso kulalikira

Zokhudza Abalewa

Tikukhulupirira kuti Yehova apitirizabe kuthandiza abale athuwa amene mwachikhulupiriro, ‘akuthamangabe’ panjira yachilungamo ngakhale akuzunzidwa.​—Oweruza 8:4.