Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Aleksey Budenchuk ndi mwana wake wamwamuna Yegor; mwana wake wamkazi, Sofiya; ndi mkazi wake, Tatyana

7 JULY, 2021
RUSSIA

M’bale Aleksey Budenchuk Watulutsidwa M’ndende ya ku Russia

M’bale Aleksey Budenchuk Watulutsidwa M’ndende ya ku Russia

Pa 6 July, 2021, M’bale Aleksey Budenchuk anatulutsidwa kundende ya mumzinda wa Orenburg nthawi yomwe amayembekezera kutulutsidwa kundendeko itakwana. Iye ndi mmodzi mwa abale 6 amumzinda wa Saratov amene anamangidwa mu September 2019. Panopa abale atatu adakali m’ndende. Anthu a m’banja la m’baleyu komanso anzake anayenda mtunda wa makilomita 800 kuti akapezeke pamene m’baleyu ankamasulidwa. Tsopano azikakhala limodzi ndi banja lake ku Saratov.