Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 25, 2020
RUSSIA

M’bale Alushkin ndi a Mboni Enanso 5 ku Russia Awina Apilo pa Chigamulo cha Khoti Laling’ono

M’bale Alushkin ndi a Mboni Enanso 5 ku Russia Awina Apilo pa Chigamulo cha Khoti Laling’ono

Pa 25 March, 2020, khoti la m’chigawo cha Penza linagamula mokomera M’bale Vladimir Alushkin, Vladimir Kulyasov, Andrey Magliv, ndi M’bale Denis Timoshin, kuphatikizaponso Mlongo Tatyana Alushkina ndi Mlongo Galiya Olkhova. Milandu ya a Mboniwa ikuyenera kuzengedwanso.

Chifukwa chowina apilo imeneyi, M’bale Alushkin atulutsidwa m’ndende masiku akubwerawa. M’baleyu komanso abale ndi alongo enawo apitirizabe kutsatira zomwe anauzidwa kuti asamachite pamene akudikira kuti milandu yawo izengedwenso.