Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Anatoliy Tokarev ndi mwana wake wamwamuna Andrey, mkazi wake Margarita ndiponso mwana wake wamkazi Yekaterina

OCTOBER 8, 2020
RUSSIA

M’bale Anatoliy Tokarev Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka Zitatu ndi Hafu ku Russia

M’bale Anatoliy Tokarev Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka Zitatu ndi Hafu ku Russia

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 23 October 2020, * khoti la m’boma la Oktyabrsky ku Kirov lidzapereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Anatoliy Tokarev. Khoti likhoza kudzagamula kuti akakhale kundende zaka zitatu ndi hafu.

Zokhudza M’baleyu

Anatoliy Tokarev

  • Chaka chobadwa: 1958 (Ku Baranovskaya, M’chigawo cha Kirov)

  • Mbiri yake: Analeredwa ndi mayi ake. Anali injiniya wa mapulogalamu apakompyuta koma pano anapuma pa ntchito. Amakonda kujambula zithunzi, kusewera tchesi komanso kuimba kodiyoni. Mu 1979 anakwatirana ndi Margarita. Ali ndi ana awiri

  • Anasiya kukhulupirira zoti kuli Mulungu pambuyo pochita maphunziro a sayansi. Koma ali ndi zaka 27, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anazindikira kuti zimene Baibulo limaphunzitsa sizimatsutsana ndi sayansi

Mlandu Wake

Pa 24 May 2019, apolisi ochokera kugulu lothana ndi anthu ochita zinthu zoopsa (Russia’s Center for Countering Extremism), anakathyola n’kulowa m’nyumba ya a Tokarev. Apolisiwo anayamba kupanikiza M’bale Tokarev ndi mafunso. Iwo anaopseza kuti amanga banja la M’bale Tokarev ngati savomereza kuti amachita “zinthu zoopsa.” Kenako, anamutengera kudipatimenti yofufuza milandu kuti akamufunse mafunso.

Patatha miyezi pafupifupi 5, M’bale Tokarev anauzidwa kuti wapalamula mlandu wochita zinthu zosemphana ndi magawo awiri m’Buku la Malamulo a Zaupandu la dziko la Russia. M’baleyu akuimbidwa mlandu wopereka ndalama zothandizira gulu lochita “zinthu zoopsa.” Oimira boma pa mlanduwu akugwiritsanso ntchito zomwe anajambula mobisa atapita kunyumba ya a Tokarev monga umboni wotsimikizira kuti a Anatoliy anakonza msonkhano ndipo pamsonkhanowo anthu amagwiritsa ntchito mabuku olimbikitsa “zinthu zoopsa” omwe analetsedwa.

Tikupempherera M’bale Tokarev ndi banja lake. Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza ‘kuwachitira zinthu mokhulupirika.’—Salimo 18:25.

^ ndime 3 Detili likhoza kusinthidwa