APRIL 7, 2021
RUSSIA
M’bale Anatoliy Vilitkevich Akuyembekezera Chigamulo Cha Mlandu Wake Ndipo Akupitirizabe Kukhala Wokhulupirika
Tsiku Lopereka Chigamulo
Khoti la M’Boma la Leninskiy la mu mzinda wa Ufa, posachedwapa lipereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Anatoliy Vilitkevich. a Loya woimira boma pa mlanduwu, sananenebe chilango chimene m’baleyu akuyenera kulandira.
Zokhudza M’baleyu
Anatoliy Vilitkevich
Chaka Chobadwa: 1986 (M’dera la Khabarovsk)
Mbiri Yake: Amagwira ntchito ya ukalipentala. Anakwatirana ndi Alyona mu 2008. Amakonda kupita kokayenda ku nkhalango n’kukagonera komweko.
Ali mwana, makolo ake anamuthandiza kuti azikonda Mlengi. Iye amasangalala kwambiri ndi lonjezo lakuti tsiku lina, anthu adzakhala limodzi ndi zinyama mwamtendere. Anabatizidwa mu 1997 ali ndi zaka 11.
Mlandu Wake
Pa 8 August 2018, M’bale Anatoliy Vilitkevich anaikidwa pa mndandanda wa anthu omwe ankawaganizira kuti ndi anthu oopsa ku Russia. M’bale Anatoliy pamodzi ndi M’bale Dennis Christensen, anali Amboni oyambirira kutsekeredwa m’ndende Khoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia litaletsa gulu la Mboni za Yehova mu April 2017. Abalewa anawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.
Apolisi anaika makamera m’nyumba ya Anatoliy ndi Alyona. Malinga ndi zimene anapeza, apolisiwo anati Anatoliy ali ndi mlandu chifukwa chakuti iwowo limodzi ndi anzawo ena ankakambirana nkhani zokhudza Baibulo m’nyumba mwawo. Panopa m’baleyu akuimbidwa mlandu woti ankatsogolera pa zokambirana ndi gulu lomwe apolisiwo amati ndi lochita zinthu zoopsa.
Pa nthawi imene apolisi ankatenga m’bale Anatoliy, mmodzi wa apolisiwo analankhula mwamwano kuuza Alyona yemwe ndi mkazi wa m’baleyu kuti “apeze mwamuna wina.” Anatoliy anafotokoza zimene zinachitika panthawi imene apolisi ankawafunsa mafunso. Iwo anati, “Ndinali ndi nkhawa kwambiri komanso ndinkavutika maganizo. Apolisiwo anandiuza kuti ngati sindivomera mlanduwo ndiye kuti mkazi wanga ndiponso anthu amene ankachita misonkhano m’nyumba mwathu alangidwa koopsa. Ankandiuza mobwerezabwereza kuti mkazi wanga akamutsekera kundende. Pa nthawi ngati zimenezi, ndinkapemphera kwa Yehova kuti andipatse mtendere wamumtima.”
Anatoliy akhala miyezi yoposa iwiri m’ndende kuyembekezera kuzengedwa mlandu. Akhalanso miyezi yoposa 9 pa ukaidi wosachoka pakhomo komanso atha chaka ndi hafu atauzidwa kuti sakuloledwa kutuluka m’dzikolo. Ali m’ndende, analemba m’buku lawo zitsanzo za anthu a m’Baibulo omwenso ankazunzidwa. Iwo anati: “Ndikukumbukira kuti sikuti Yehova ankawateteza anthuwa kuti asakumane ndi mavuto, komabe iye sanawasiye okha. Zimenezi zinkandilimbitsa kwambiri komanso kundithandiza kuona kuti nanenso Yehova sandisiya ndekha. Ndinkadziwa kuti chofunika n’kupitiriza kukhala wokhulupirika.” Makalata amene mkazi wake ankamulembera ankamulimbikitsanso kwambiri. Iye anati “Pa makalata amene Alyona anandilembera koyambirira, m’kalata yake ina anaikamo zithunzi zambirimbiri zimene tinajambulitsa tili ndi anzathu. Madzulo alionse ndinkatenga zithunzizi n’kumayesetsa kukumbukira zinthu zosangalatsa zimene zinachitikira ineyo ndi munthu aliyense amene ali pachithunzipo. Zimenezi zinkandithandiza kuona kuti anzangawo ndili nawo limodzi.”
Anatoliy ndi Alyona akupitirizabe kukhala okhulupirika ndipo chitsanzo chawo n’cholimbikitsa kwambiri kwa tonsefe. Ndife osangalala kuti abale ndi alongo athu ku Russia ndi olimba mwauzimu ngakhale kuti akuzunzidwa koopsa. Tikuthokoza Yehova chifukwa chomvetsera mapemphero a abale ndi alongo tonse, opempherera abale athuwa.—2 Akorinto 1:11.
a Nthawi zambiri zimakhala zovuta kudziwa tsiku limene a khoti angapereke chigamulo.