Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Andrey Gubin

5 APRIL, 2021
RUSSIA

M’bale Andrey Gubin Akupitirizabe Kukhala Wokhulupirika Pamene Akukumana ndi Mayesero

M’bale Andrey Gubin Akupitirizabe Kukhala Wokhulupirika Pamene Akukumana ndi Mayesero

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la m’Boma la Birobidzhan, lomwe lili m’dera lachiyuda loima palokha, posachedwapa lilengeza chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Andrey Gubin. *

Zokhudza M’baleyu

Andrey Gubin

  • Chaka chobadwa: 1974 (Mumzinda wa Saran m’dziko la, Kazakhstan)

  • Mbiri Yake: Ali ndi mchimwene komanso mchemwali wake. Atamaliza sukulu ali wachinyamata, anayamba kugwira ntchito yokonza maloko kuti azithandiza banja lawo. Kenako anayamba kugwira ntchito yoyendetsa magalimoto akukuakulu komanso makina odulira zitsulo ndi matabwa. Amakonda kuchita masewera, kulemba ndakatulo komanso kuimba nyimbo

  • Kungoyambira ali mwana, ankada nkhawa ndi zinthu zoipa komanso zopanda chilungamo zimene zimachitika m’dzikoli. Koma atayamba kuphunzira Baibulo anapeza mtendere ndipo anayamba kukhala ndi moyo wosangalala. Zimene Baibulo linalonjeza, zoti padzikoli padzakhala chilungamo komanso mtendere, zinamulimbikitsa kuti adzipereke kwa Yehova, ndipo kenako anabatizidwa mu 1991 ali ndi zaka 17. Kenako anakwatirana ndi Tatyana mu 2007 ndipo mu 2011 anasamukira ku Birobidzhan

Mlandu Wake

Pa 12 February 2020, apolisi a gulu lachitetezo la FSB anayamba kufufuza m’Bale Andrey Gubin, ndipo pa 17 September, 2020 mlandu wake unayambika.

Mlandu wa m’baleyu ndi umodzi mwa milandu 19 imene abale ndi alongo athu a ku dera loima palokha la Ayuda akuimbidwa. Mlandu umenewu ndi umodzi mwa milandu imene apolisi anatsegula atachita chipikisheni nyumba zambiri. Apolisiwo anatchula ntchito imeneyi anaitchula kuti “Tsiku la Chiweruzo.” Pa 17 May 2018, apolisi okwana 150 anapanga chipikisheni m’nyumba 22 za a Mboni za Yehova. Apolisiwo analandanso makadi akubanki, ndalama, zinthuzi, makompyuta komanso mafoni.

Panopa apolisi aletsa M’bale Andrey ndi mkazi wake kugwiritsira ntchito ma akaunti awo akubanki moti zimenezi zachititsa kuti akumane ndi vuto lalikulu la zachuma. Banjali lakhala likuzunzidwa kwa miyezi ingapo ndipo zimenezi zakhudza kwambiri thanzi la mlongo Tatyana. Koma chinthu chimene chawathandiza kwambiri ndi kuwerenga Baibulo nthawi zonse. Iwo alimbikitsidwanso kwambiri ndi malangizo a m’Baibulo okhudza zimene zingatithandize kupirira tikakumana ndi mavuto aakulu.

Chikhulupiriro cha M’bale Andrey mwa Yehova komanso gulu lake chalimba kwambiri chifukwa cha zimene abale ndi alongo mumpingo akuchita powathandiza. Mwachitsanzo tsiku lina M’bale Andrey ankada nkhawa kwambiri ndi zimene akukumana nazo. Ndiye anaganiza zoti afotokozere m’bale wina amenenso akuzengedwa mlandu. Choyamba m’baleyo anamutsimikizira Andrey kuti sizachilendo kukhala ndi nkhawa chifukwa cha zimene tikukumana nazo. Kenako anamukumbutsa kuti Yesu ankaona kuti ndi mwayi kuzunzidwa chifukwa cha dzina la Yehova. M’bale Andrey ananena kuti, “Pambuyo pa zimenezi, mtima wanga unakhala m’malo. Panopa ndatsimikiza mtima kuti ndipitirizabe kuchita chifuniro cha Atate wathu.”

Pemphero lathu ndi lakuti M’bale Andrey ndi Mlongo Tatyana apitirizebe kudalira Mawu a Mulungu komanso abale ndi alongo athu kuti aziwalimbikitsa komanso kuwathandiza kukhala olimba. Sitikukayikira kuti “anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino.”—Mlaliki 8:12.

^ Nthawi zina n’zovuta kudziwiratu deti lopereka chigamulo.