Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Andrzej Oniszczuk ali muselo ya m’khoti pamene nthawi yake yoti akhale m’ndende inkaonjezeredwa posachedwapa

AUGUST 9, 2019
RUSSIA

M’bale Andrzej Oniszczuk Wakhala M’ndende Yayekha Pafupifupi Chaka Chimodzi

M’bale Andrzej Oniszczuk Wakhala M’ndende Yayekha Pafupifupi Chaka Chimodzi

M’bale Andrzej Oniszczuk yemwe ndi nzika ya dziko la Poland, wakhala ali m’ndende ku Russia poyembekezera kuzengedwa mlandu kungoyambira pamene anamangidwa ndi apolisi pa 9 October, 2018. Posachedwapa nthawi yake yoti akhale m’ndende inawonjezeredwa kwa ulendo wa nambala 5. Nthawi yake yatsopano yoti akhale m’ndende idzatha pa 2 October, kutangotsala masiku ochepa kuti akwanitse chaka chimodzi ali m’ndende.

M’bale Oniszczuk asanamangidwe ali limodzi ndi mkazi wake Anna. Kungochokera pamene mwamuna wake anamangidwa miyezi 10 yapitayo, Anna sanaloledwepo kupita kukamuona

Kungoyambira pamene anamangidwa, M’bale Oniszczuk wakhala akusungidwa m’ndende yayekha. M’baleyu saloledwa kugona kuti apumule kuyambira 6 koloko m’mawa mpaka 9 koloko usiku. Amangololedwa kusamba madzi otentha kwa maminitsi 15 kamodzi kokha pa mlungu. Kwa miyezi 10 imene m’baleyu wakhala ali m’ndende, mkazi wake dzina lake Anna sanaloledwepo kupita kukamuona. Amalumikizana naye polemba makalata basi. Anna wakhala akupempha kambirimbiri kuti azimulola kupita kukaona mwamuna wake koma nthawi zonse amakanizidwa.

Monga mmene nkhani ina inanenera m’mbuyomu, M’bale Oniszczuk anamangidwa pamene apolisi a mumzinda wa Kirov ndi apolisi apadera ovala zobisa nkhope anakachita chipikisheni m’nyumba yake komanso m’nyumba zina 18 za mumzindawu. M’bale Oniszczuk anamutsegulira mlandu chifukwa choimba nyimbo za Ufumu komanso kuphunzira mabuku a chipembedzo chake.

Abale enanso 4 ochokera ku Kirov (a Maksim Khalturin a zaka 44, a Vladimir Korobeynikov a zaka 66, a Andrey Suvorkov a zaka 26, komanso a Evgeniy Suvorkov a zaka 41) anamangidwa chaka chatha limodzi ndi M’bale Oniszczuk ndipo anaikidwa m’ndende poyembekezera kuzengedwa milandu. Abalewa akhala ali paukaidi wosachoka panyumba kungoyambira nthawi imeneyo. Panopa M’bale Oniszczuk komanso abale 4 enawo akuyembekezera chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe.

Chaka chino, akuluakulu a boma la Russia anatsegulira milandu abale enanso oposa 7 ochokera ku Kirov ndipo wamkulu kwambiri pa onse ndi M’bale Yevgeniy Udintsev yemwe ali ndi zaka 70. Panopa a Mboni za Yehova 12 ku Kirov akuimbidwa milandu chifukwa chochita zimene amakhulupirira.

Ponena za M’bale Oniszczuk, Anna komanso abale athu okondedwa ena onse ku Russia, tiyeni tisaiwale zimene mawu ouziridwa awa amatikumbutsa kuti: “Kumbukirani amene ali m’ndende ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi. Kumbukiraninso amene akuzunzidwa, popeza inunso mudakali m’thupi lanyama.”—Aheberi 13:3.