11 OCTOBER 2024
RUSSIA
M’bale Arsen Avanesov Watulutsidwa M’ndende ku Russia
Pa 9 October 2024, M’bale Arsen Avanesov anatulutsidwa m’ndende ku Russia. Pamene ankamuzenga mlandu pa 29 July 2021, anamupeza kuti ndi wolakwa ndipo anamugamula kuti akakhale m’ndende kwa zaka 6 ndi hafu. Atapanga apilo, oweruza anawonjezera nthawi yomwe akakhale m’ndende ndipo inafika pa zaka 7. Chifukwa choti anali atakhala kale kundende kwa zaka ziwiri asanagamulidwe, panopa wamaliza nthawi yonse imene amayenera kukhala m’ndende.
Bambo ake, M’bale Vilen Avanesov, omwe nawonso anapezeka wolakwa pa mlandu womwewo, anagamulidwa kuti akakhale m’ndende kwa zaka 6. Iwo anatulutsidwa pa 9 February 2024.
Arsen anakhalabe wolimba pamene anali m’ndende chifukwa anali wodzipereka kwa Yehova. M’mawu ake omaliza omwe analankhula kukhoti asanapite kundende ananena kuti: “Ndinalonjeza Yehova kuti ndidzakhalabe wokhulupirika kwa iye. Ndinapereka moyo wanga kwa Yehova ndipo ndinachita zimenezi kuchokera pansi pa mtima. Sindikufuna, sindingachite ndipo sindidzalephera kukwaniritsa zimene ndinalonjeza kwa Yehova.” Arsen ananenanso kuti chikhulupiriro chake chomwe chinazika kwambiri mizu sichingachepe. Iye ananena kuti: “Chikhulupiriro changa sichinagwedezekepo, ndipo panopa chalimba kwambiri.”
Tikusangalala kwambiri kuti tsopano M’bale Arsen wakumananso ndi anthu a m’banja lake ndipo tipitiriza kupempherera mosalekeza abale ndi alongo athu onse omwe adakali m’ndende. Ndi zolimbikitsa kudziwa kuti ngakhale kuti tonsefe ‘tikukumana ndi mayesero osiyanasiyana,’ koma chifukwa choti tikupitirizabe kupirira komanso kukhalabe ndi chikhulupiriro, tidzadalitsidwa kwambiri.—1 Petulo 1:6, 7.