Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: M’bale Sergey Britvin ndi M’bale Vadim Levchuk ali muselo ya m’khoti

AUGUST 20, 2020
RUSSIA

M’bale Britvin ndi Levchuk Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 6 ndi Hafu ku Russia

M’bale Britvin ndi Levchuk Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 6 ndi Hafu ku Russia

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 2 September 2020, * ku Khoti la Mumzinda wa Berezovsky m’Chigawo cha Kemerovo

Chigamulo Chomwe Chingadzaperekedwe

Zaka 6 ndi hafu m’ndende

Zokhudza Abalewa

Sergey Britvin

  • Chaka Chobadwa: 1965 (m’Chigawo cha Kemerovo)

  • Mbiri yake: Kwa zaka zambiri wakhala akugwira ntchito yoyendetsa thiraki komanso mashini okwezera zinthu m’mwamba. Anapuma msanga pantchito chifukwa chodwaladwala. Amakonda kuchita masewera olimbitsa thupi

  • Anakwatira a Natalya mu 1992. Anayamba kuphunzira Baibulo mu 1995 pambuyo pophunzira zimene Mulungu analonjeza kuti akufa adzauka. Patapita zaka zambiri, a Natalya anaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo. Anachita chidwi kwambiri ndi chikhulupiriro cha amuna awo a Sergey komanso mmene Baibulo linawathandizira kukhala ndi makhalidwe ambiri abwino

Vadim Levchuk

  • Chaka Chobadwa: 1972 (m’Chigawo cha Kemerovo)

  • Mbiri yake: Anakulira m’banja losapembedza Mulungu. Ankagwira ntchito mumgodi kwa zaka 14

  • Anayamba kuphunzira Baibulo mu 1992. Anakwatira a Tatiana mu 1997. Ali ndi ana aamuna awiri. Onse m’banja lawo amalemekeza mfundo za m’Baibulo. Amakondanso masewera olimbitsa thupi komanso kuchita zinthu zina zosiyanasiyana

Milandu Yawo

Pa 22 July 2018, apolisi a gulu lachitetezo (FSB) anathyola ndi kulowa m’nyumba 8 za abale athu mumzinda wa Berezovsky. Izi zinachititsa kuti apolisiwo amange M’bale Britvin ndi M’bale Levchuk komanso kuwapanikiza ndi mafunso. Kenako khoti la m’Boma la Kemerovo linagamula kuti abalewa akakhale kaye kundende poyembekezera kuwazenga mlandu. Abalewa anakhaladi m’ndendemo kwa pafupifupi chaka ndi hafu. Pa 25 December 2019, anawasamutsa kuti akhale pa ukaidi wapanyumba ndipo akugwirabe ukaidiwu mpaka pano.

M’bale Britvin ndi M’bale Levchuk ali m’gulu la abale 5 omwe akuimbidwa mlandu m’Chigawo cha Kemerovo chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Nthawi zonse timaganizira ndi kupempherera abale ndi alongo athu onse omwe akumangidwa ku Russia. Paja lemba la Aheberi 13:3 limatikumbutsa kuti: “Kumbukirani amene ali m’ndende ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi. Kumbukiraninso amene akuzunzidwa, popeza inunso mudakali m’thupi lanyama.”

^ ndime 3 Detili likhoza kusinthidwa