Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 11, 2020
RUSSIA

M’bale Dennis Christensen Amuchotsa Muselo Yapadera Ndipo Apita Naye Kumene Kuli Akaidi Ena

M’bale Dennis Christensen Amuchotsa Muselo Yapadera Ndipo Apita Naye Kumene Kuli Akaidi Ena

Pa 11 July 2020, akuluakulu akundende ya ku Lgov, anasamutsa M’bale Christensen n’kupita naye kumene kuli akaidi ena. Anamuchotsa muselo ina yozunzira anthu, momwe wakhalamo masiku 15 apitawa. Monga tinanenera kale, anamuika museloyi pamilandu yochita kumunamizira. Koma panopa ali kumalo kumene kumakhala akaidi ena. M’baleyu akusangalala ndithu ndipo sakuoneka wankhawa. Amene akumuimira pa mlandu wake akufuna kukachita apilo milandu imene akuimbidwa panopa ndipo akukhulupirira kuti zimenezi sizilepheretsa pempho loti atulutsidwe msanga.