Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Dmitriy Terebilov ndi mkazi wake, Irina

AUGUST 5, 2021
RUSSIA

M’bale Dmitriy Terebilov Akhoza Kumangidwa ka Nambala 5, Ndipo Kakhala Koyamba Kumangidwa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

M’bale Dmitriy Terebilov Akhoza Kumangidwa ka Nambala 5, Ndipo Kakhala Koyamba Kumangidwa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Zimene Zinachitika

  1. Khoti la m’boma la Sverdlovskiy mumzinda wa Kostroma likuyembekezeka kulengeza chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Dmitriy Terebilov. * Khotilo likhoza kugamula kuti akakhale kundende zaka 5

  2. 8 September 2020

    Mlandu wa M’bale Dmitriy unayamba

  3. 25 May 2020

    A Dmitry anayamba kuimbidwa mlandu komanso analetsedwa kuyenda maulendo ena

  4. 9 September 2019

    Ma akaunti awo akubanki anatsekedwa

  5. 13 June 2019

    Anawatsegulira mlandu wogawa mabuku omwe ndi oletsedwa komanso wopezeka pamisonkhano ya gulu lomwe ndi loletsedwa

  6. 25 July 2018

    Apolisi anakafufuza m’nyumba mwa a Dmitry pamene iwo ndi mkazi wawo anali kumsonkhano ku Moldova. Atangofika kunyumba anawamanga komanso kuwapanikiza ndi mafunso

Zokhudza M’baleyu

Pamene a Dmitriy akupitiriza kukhala ndi chimwemwe chimene chimabwera pomwe “akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu,” tikukhulupirira kuti “mzimu waulemerero, umene ndi mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa” iwo.—1 Petulo 4:14.

^ N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo.