Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pa 21 January 2021, wakumana ndi mkazi wake Yevgeniya panja pa siteshoni ya sitima ku Uzbekistan, pambuyo potulutsidwa m’ndende ku Russia

21 JANUARY 2021
RUSSIA

M’bale Feliks Makhammadiyev Watulutsidwa M’ndende N’kutumizidwa ku Uzbekistan

M’bale Feliks Makhammadiyev Watulutsidwa M’ndende N’kutumizidwa ku Uzbekistan

Pa 31 December 2020, M’bale Feliks Makhammadiyev anatulutsidwa m’ndende ya ku Russia. Khoti la m’boma la Belyayevsky m’chigawo cha Orenburg linagamula kuti asungidwe kaye kwa kanthawi kumalo ena mpaka atapatsidwa zikalata zomuyenereza kuti athe kubwerera kwawo ku Uzbekistan. Anachita zimenezi chifukwa choti mu April 2020, boma la Russia linalanda ziphaso zake za unzika. Pa 20 January 2021, apolisi anamukwezetsa sitima yopita kwawo ku Uzbekistan. Ndife osangalala kukudziwitsani kuti M’bale Makhammadiyev anayenda bwino ndipo anafika ku Uzbekistan pa 21 January 2021. Mkazi wake Yevgeniya anafika ku Uzbekistan pa 19 January 2021 ndipo pamene mwamuna wakeyu ankafika anapita kukamulandira.

M’bale Makhammadiyev anakhala ku Russia zaka 18. Mu 2002, M’bale Makhammadiyev ali ndi zaka 17 anasamuka limodzi ndi mayi ake kuchoka ku Uzbekistan kupita ku Saratov ku Russia. Mu 2004, anabatizidwa ali ndi zaka 19. Mu 2011, anakwatirana ndi Yevgeniya.

Pa 12 June 2018, apolisi onyamula zida komanso ovala zotchinga nkhope a gulu la FSB anathyola ndi kulowa m’nyumba ya Feliks ndi Yevgeniya Makhammadiyev. M’bale Makhammadiyev anamangidwa ndipo anakhala m’ndende chaka chimodzi poyembekezera kuti mlandu wawo uzengedwe. Nthawi zonse ankapemphera kwa Yehova kuti awathandize kukhala ndi mphamvu. Iwo akufotokoza kuti: “Tsiku lililonse ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuti ndipeze mtendere ndi chimwemwe pa tsikulo.”

Patangodutsa milungu iwiri kuchokera pamene M’bale Makhammadiyev anamenyedwa kwambiri ndi asilikali kundende

Kenako pa 19 September 2019, M’bale Makhammadiyev komanso abale ena 5 anagamulidwa kuti onse ndi olakwa ndipo akuyenera kupita kundende. Iwo anachita apilo za nkhaniyi. Komabe, khoti linakana zomwe abalewa anapempha ndipo m’baleyu ndi abale ena 4 anatumizidwa kundende ya ku Orenburg yomwe ili pamtunda wopitirira makilomita 800, kuchokera kwawo ku Saratov. Abalewa atangofika kundende ya ku Orenburg anamenyedwa kwambiri.

Ngakhale kuti akukumana ndi mavuto onsewa, m’baleyu akupitiriza kukhala wosangalala. Mkazi wake anati: “Ndikusangalala kwambiri ndi zomwe mwamuna wanga wachita. Anayesetsa kupirira komanso kuchita zinthu mwaulemu pamene mlandu wake unkazengedwa m’khoti ndipo akupitirizabe kuchita zimenezi. Ndipo akundithandizanso kuti nane ndizipirira.”

Ngakhale kuti akuluakulu a boma ku Russia anamuchitira nkhanza n’cholinga choti asiye kukhala wokhulupirika, iye ananena kuti nkhanza zomwe anamuchitirazo zinamuthandiza kuti alimbitse chikhulupiriro chake mwa Yehova. Zimenezi zikutikumbutsa mawu omwe Yosefe anauza abale ake pa Genesis 50:20 kuti: “Inu munali ndi cholinga chondichitira zoipa. Koma Mulungu anali ndi cholinga chabwino.”