Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Gennady Shpakovskiy, atangotulutsidwa kumene ali ndi mkazi wake Tatiana, ndi mwana wake Maria

AUGUST 3, 2020
RUSSIA

M’bale Gennady Shpakovskiy Watulutsidwa Mundende

M’bale Gennady Shpakovskiy Watulutsidwa Mundende

Lolemba pa 3 August 2020, khoti la m’chigawo cha Pskov linagamula kuti M’bale Gennady Shpakovskiy atulutsidwe mundende. Khotili linasintha chigamulo chimene m’baleyu anapatsidwa choti akhale mundende zaka 6 ndi hafu. M’malomwake, linagamula kuti akuyenera kutsatira malamulo omuletsa kuchita zinthu zina pazaka zimenezi koma asakhale mundende. Kenako patangodutsa maola ochepa, M’baleyu anamutulutsa mundende. Mbali ya boma ili ndi ufulu wopanga apilo chigamulochi.