JUNE 5, 2020
RUSSIA
M’bale Gennady Shpakovskiy ku Russia Akhoza Kuikidwa M’ndende Zaka 7 ndi Hafu
Khoti la mumzinda wa Pskov lidzapereka chigamulo chake pa 8 June 2020, chokhudza mlandu wa M’bale Gennady Shpakovskiy yemwe ali ndi zaka 61. M’baleyu akuganiziridwa kuti anachita “zinthu zoopsa” chifukwa choti anapezeka akuchititsa misonkhano yampingo m’kagulu ka anthu ochepa kunyumba kwake. Amene akumuimba mlanduwu anapempha khoti kuti lidzagamule kuti M’bale Shpakovskiy akhale m’ndende zaka 7 ndi hafu.
Chakumayambiriro kwa chaka cha 2018, gulu la apolisi a FSB linayamba kufufuza mwamseri banja la a Shpakovskiy. Kwa miyezi ingapo, apolisiwo ankamvetsera mobisa zilizonse zomwe banjali linkakambirana m’nyumba mwawo ndiponso ankaona zimene ankachita. Tsiku lina pa 3 June 2018, nthawi ya 12:45 masana, gulu la FSB ndiponso apolisi a National Guard onyamula mfuti anafika n’kuthyola chitseko cha nyumba ya m’baleyu. M’nyumbayi munali a Mboni omwe anasonkhana mwamtendere. Kenako apolisiwo anachita chipikisheni kwa maola 6.
Ndiyeno gulu la FSB linalanda matabuleti ndi mafoni kenako a Mboniwo anatengedwa kuti akawafunse mafunso. Atafika kokawafunsa mafunso, apolisi anawalankhula mawu onyoza ndiponso kuwaopseza kuti akhoza kuchotsedwa ntchito komanso kuikidwa m’ndende. M’bale Shpakovskiy anafunsidwa mafunso mpakana 10 koloko usiku.
Pa 19 March 2019, M’bale Shpakovskiy anauzidwa kuti ali ndi mlandu wotsogolera ntchito za gulu “lochita zinthu zoopsa.” Patatha miyezi 5, m’baleyu anauzidwanso kuti anapalamula mlandu winanso “wopereka ndalama zothandizira zinthu zoopsa.”
Pamene tikuyembekezera chigamulo cha khoti, tikupemphera mwachikhulupiriro kuti Yehova athandize banja la a Shpakovskiy kukhalabe lolimba ndipo tikudziwa kuti adzapeza mphoto akapitiriza kupirira mokhulupirika.—2 Mbiri 15:7.