Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Igor Ivashin

27 MARCH 27, 2020
RUSSIA

M’bale Igor Ivashin Akuyembekezera Kuweruzidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 7 ku Russia

M’bale Igor Ivashin Akuyembekezera Kuweruzidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 7 ku Russia

Khoti lamumzinda wa Lensky ku Sakha likuyembekezera kupereka chigamulo cha mlandu wa m’bale Igor Ivashin pa 31 March, 2020. Loya woimira boma pa mlanduwu akufuna kuti m’baleyu akakhale kundende zaka 7.

Mu February 2018, khoti lamumzinda wa Yakutsk linapereka chilolezo kwa apolisi amumzindawu kuti azimvetsera zimene M’bale Ivashin ankakambirana ndi anthu ena pafoni. Patadutsa miyezi ingapo, apolisi anakafufuza kunyumba 8 za a Mboni za Yehova, kuphatikizapo kunyumba kwa M’bale Ivashin. Apolisiwo anagwira m’baleyu limodzi ndi a Mboni ena okwana 21 ndipo anapita nawo kupolisi komwe anakafunsidwa mafunso. Kenako wachiwiri kwa loya woimira boma pamilandu, anakasuma kukhoti ndipo anatsegulira M’bale Ivashin mlandu wotsogolera kagulu “koopsa.”

Koma pa 20 November, 2019, khotilo linabweza mlanduwu ku ofesi ya loya woimira boma pamilandu chifukwa analibe umboni wokwanira wosonyeza kuti m’bale Ivashin ndi wolakwa. Ofesiyi inachita apilo mlanduwu kukhoti lomwe lija. Khotilo linayamba kumvetsera mlanduwu chakumayambiriro kwa mwezi wa February 2020.

M’bale Ivashin ndi mkazi wake, Natalia, ali ndi ana aakazi awiri. Pamene tsiku lopereka chigamulo likuyandikira, tikupempha Yehova kuti athandize anthu a m’banja la m’baleyu kuti athe “kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.”—Akolose 1:11.