Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Igor Tsarev

28 JANUARY 2021
RUSSIA

M’bale Igor Tsarev Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 4 Chifukwa Chophunzira Baibulo

M’bale Igor Tsarev Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 4 Chifukwa Chophunzira Baibulo

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 1 February 2021, * Khoti la m’Boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia, lidzalengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Igor Tsarev. M’baleyu atha kugamulidwa kuti akakhale kundende zaka 4.

Zokhudza M’baleyu

Igor Tsarev

  • Chaka chobadwa: 1974 (ku Birakan, M’dera Loima Palokha la Ayuda)

  • Mbiri yake: Ali ndi azichemwali ake awiri aang’ono kwa iye. Ali pasukulu, ankagwira ntchito yodula mitengo, ukalipentala, komanso ntchito zamagetsi kuti azithandiza banja lawo. Amakonda kukaona zinthu zam’chilengedwe ndi kuwedza nsomba

  • Anayamba kufuna kudziwa cholinga cha moyo pa nthawi yomwe ankagwira ntchito ya usilikali. Zimenezi zinachititsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo limodzi bambo ake. Choncho mu 1997, anabatizidwa. Mu 1998, anakwatirana ndi Viktoriya. Ali ndi mwana wamkazi wamng’ono

Mlandu Wake

Pa 30 July 2019, apolisi ku Russia anasumira mlandu M’bale Igor Tsarev. M’baleyu akuimbidwa mlandu woti amaphunzira Baibulo “n’cholinga choti aziphunzitsa anthu zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira.” Apolisi a gulu loona za chitetezo ku Russia (FSB), anajambula mwachinsinsi misonkhano ndipo anagwiritsa ntchito mavidiyo omwe anajambulawo ngati umboni wa zomwe M’bale Tsarev analakwitsa. N’zodabwitsa kuti woimira boma pa mlanduwu anapempha kuti mlanduwu ukamazengedwa anthu ena onse asamvetsere nawo. Iye ananena kuti ngati anthu ena angamvetsere mlanduwu atha kukopeka ndi zimene M’bale Tsarev anganene n’kukhala a Mboni za Yehova. A khoti anagwirizana ndi zimene woimira boma pa mlanduyu anapempha.

M’bale Tsarev anati: “Zomwe khoti ligamule posachedwapa zisintha moyo wanga. Ndipo n’zomwe zachitika kale. Panopa andiletsa kupita m’madera ena. Ndinkafunika kufotokozera abwana anga kuntchito chifukwa chimene apolisi akundifufuzira. Abwana anga ndi anzanga omwe ndimagwira nawo ntchito sakumvetsa chifukwa chimene akundiimbira mlandu, komabe iwo amadziwa kuti nthawi zonse Akhristu akhala akuzunzidwa.”

Tikupitirizabe kupempherera M’bale Tsarev ndi banja lake. Ndipo tikudziwa kuti Yehova awathandiza “mwa mphamvu ya mzimu wake.”—Aefeso 3:16.

^ Tsikuli likhoza kusintha.