Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Konstantin Guzev

FEBRUARY 19, 2021
RUSSIA

M’bale Konstantin Guzev Anamangidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

M’bale Konstantin Guzev Anamangidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Chigamulo

Pa 18 February 2021, khoti la mumzinda wa Birobidzhan, lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda, linagamula kuti kwa zaka ziwiri ndi hafu, M’bale Konstantin Guzev azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake. Moti pa nthawiyi iye safunikira kupita kundende.

Zokhudza M’baleyu

Konstantin Guzev

  • Chaka chobadwa: 1964 (Khabarovsk)

  • Mbiri yake: Bambo ake anali ankhanza komanso ankamwa mowa mwa uchidakwa. Iye ankafuna kudziwa cholinga cha moyo. Ndiye chifukwa chakuti sanapeze mayankho, anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa. Patapita nthawi anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Kenako anapeza mayankho a mafunso amene anali nawo. Zimenezi zinachititsa kuti asinthe kwambiri moyo wake ndipo m’chaka cha 2000 anabatizidwa. Mu 2001 anakwatira Anastasiya.

Mlandu Wake

Apolisi anakachita chipikisheni kunyumba ya a Konstantin mu May 2018. Panthawi imeneyo, apolisi okwana 150 anachita chipikisheni m’nyumba za abale ambiri mumzinda wonse wa Birobidzhan. Pa 29 July 2019, aboma anatsegulira mlandu a Konstantin. Chifukwa chakuti a Konstantin ankatsogolera misonkhano yachipembedzo, iwo ankaimbidwa mlandu “wotsogolera gulu lomwe limachita zinthu zoopsa.”

Pali milandu ya kukhoti yokwana 19 yomwe a Mboni za Yehova okwana 22 akuimbidwa m’derali ndipo umodzi ukukhudza a Anastasiya, akazi awo a Konstantin.

Kulimba mtima kwa abale ndi alongo a ku Russia kwathandiza a Konstantin ndi akazi awo a Anastasiya kuti nawonso akhale olimba. A Konstantin ananena kuti: “Ndaonapo komanso ndamvapo alongo ena omwe poyamba ankanena kuti sangakwanitse kulankhula m’khoti. . . . Koma ndi thandizo la Yehova komanso mapemphero a abale, iwo anakwanitsa kulankhula bwino kwambiri za chikhulupiriro chawo m’khoti.”

Tikupempherera abale ndi alongo athu onse ku Russia. Tili ndi chikhulupiriro kuti zinthu zonse zimene anthu akuchita zofuna kulepheretsa abalewa kukhalabe okhulupirika, sizidzatheka chifukwa Yehova ali nawo.—Yesaya 8:10.