Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Roman Baranovskiy ndi mayi ake, Mlongo Valentina Baranovskaya

29 JANUARY 2021
RUSSIA

M’bale Roman Baranovskiy ndi Mayi Ake, Mlongo Valentina Baranovskaya, Akuimbidwa Mlandu ku Russia

M’bale Roman Baranovskiy ndi Mayi Ake, Mlongo Valentina Baranovskaya, Akuimbidwa Mlandu ku Russia

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 1 February 2021, a Khoti la Mumzinda wa Abakan ku Republic of Khakassia likhoza kudzapereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Roman Baranovskiy ndi mayi ake, Mlongo Valentina Baranovskaya. Loya woimira boma pa mlanduwu sanapemphebe chilango chimene akufuna kuti m’bale ndi mlongoyu apatsidwe.

Zokhudza M’bale ndi Mlongoyu

Roman Baranovskiy

  • Chaka chobadwa: 1974 (Ku Balakovo, m’Chigawo cha Saratov)

  • Mbiri yake: Amagwira ntchito yokonza nyumba za anthu kuti athandize mayi ake komanso iyeyo. Amakonda kuimba gitala, kusewera tchesi ndi mpira

    Ali wachinyamata, ankafuna kudziwa cholinga cha moyo. Iye anati: “Nthawi zina ndinkapempha Mulungu kuti andithandize kudziwa cholinga cha moyo.” Mu 1993, anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo anabatizidwa mu 1997

Valentina Baranovskaya

  • Chaka chobadwa: 1951 (Ku Vannovka, Kazakhstan)

  • Mbiri yake: Anagwirapo ntchito yowerengetsera ndalama komanso yokonza mapulani azachuma mpaka pamene anapuma pa ntchitoyi mu 2006. Amakonda kuphika komanso kulemba nyimbo ndi ndakatulo

    Mu 1995, iye limodzi ndi mwana wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Anasangalala kwambiri atadziwa mfundo yakuti Mulungu sanama. Anabatizidwa mu 1996

Mlandu Wawo

Usiku wa pa 10 April 2019, apolisi onyamula mfuti ku Abakan anakachita chipikisheni kunyumba 4, kuphatikizapo ya M’bale Roman Baranovskiy ndi mayi ake a Valentina. Apolisiwa anawalanda Mabaibulo, zipangizo zamakono ndi zinthu zina. Kenako anakawatsegulira mlandu.

A Roman anati: “Pa nthawi imene apolisiwa anafika kunyumba zathu tinali tili kumisonkhano ndipo tinali titangomaliza kukambirana lemba la 1 Akorinto10:13. Tinakambirana mfundo yofunika kwambiri yakuti Yehova si amene amachititsa mayesero . . . Iye saganiza kuti: ‘Popeza kuti ndiwe wolimba, sungavutike kupirira mayeserowa pawekha. Koma popeza kuti ndiwe wofooka, ndikuthandiza kupirira mayeserowa.’ Zikanakhala choncho ndiye kuti tikanangofunikira mphamvu zathu zokha kuti tithe kupirira mayesero. Aliyense akhoza kukumana ndi mayesero. Koma tikamadalira mphamvu za Yehova, tonsefe tingathe kupirira mayesero.”

Mu July 2020, a Valentina anadwala matenda a sitiroko. Iwo anati: “Pamene thupi langa linkafooka kwambiri, m’pamenenso ndinkaona kuti Yehova akundithandiza. Zimenezi zinkachitika chifukwa chakuti sindinasiye kupemphera ndipo zinkachita kuoneratu kuti Yehova ali pafupi nane. Ndinkaona kuti ndili ndi mtendere wamumtima ndipo mawu akundisowa oti ndifotokozere bwinobwino mmene ndinkamvera.

Zinthu zimene a Valentina anakumana nazo zawathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova. Iwo anati: “Ndine wotsimikiza mtima kuti ndipitirizabe kutumikira Atate wanga komanso sindisiya kukhala wokhulupirika kaya ndikumane ndi mavuto otani pa moyo wanga.”

A Roman ananena kuti kuganizira mozama zitsanzo zotchulidwa m’Baibulo za atumiki okhulupirika amene anapirira komanso za abale ndi alongo masiku ano, zawathandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Akamaganizira zitsanzo zimenezi, nthawi zambiri amadzifunsa kuti: ‘Kodi ndi mayesero ati amene ankafunika kuwapirira, nanga n’chifukwa chiyani? N’chiyani chinawathandiza kuti asasiye kukhala okhulupirika kwa Yehova? Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji mzimu woyera powathandiza?’ Mayankho a mafunso amenewa athandiza a Roman kupitiriza kukhulupirira kuti kaya akumane ndi mavuto otani, “Yehova adzawapatsa mphamvu zoposa zachibadwa kuti akwanitse kupirira.”

Tikupemphera kuti a Roman, a Valentina komanso abale ndi alongo athu onse ku Russia apitirize kuona Yehova kukhala pothawirapo pawo ndi mphamvu zawo.—Salimo 46:1.

a Tsikuli likhoza kusintha.