JANUARY 19, 2021
RUSSIA
M’bale Sergey Britvin ndi M’bale Vadim Levchuk Adakali Okhulupirika Ngakhale Aluza Apilo
Pa 19 January 2021, Khoti la m’Chigawo cha Kemerovo linakana apilo ya M’bale Sergey Britvin ndi M’bale Vadim Levchuk. Zimenezi zikutanthauza kuti chigamulo choti akakhale kundende zaka 4 chimene khoti linapereka poyamba chiyamba kugwira ntchito. Kwa zaka zoposa zitatu, abalewa anakhala kaye m’ndende poyembekezera kuti mlandu wawo uzengedwe, choncho panopa akuyenera kugwira ukaidi kwa nthawi yosakwana chaka chimodzi. Iwo ndi otsimikiza mtima kuti apitirizabe kuchita zinthu mokhulupirika ngakhale kuti akukumana ndi mavuto amenewa.
Pa nthawi imene khoti linkapereka chigamulo choyamba, abalewa analankhula molimba mtima kuti amakhulupirira Yehova ndiponso anafotokoza mmene wawathandizira chifukwa chomutumikira.
A Britvin analankhula pamaso pa khoti kuti: “Kodi amene akuimira boma pa mlanduwu akufuna kuti ndichite chani? Akufuna kuti ndisiye kukhulupirira Yehova? Komatu kukhulupirira Yehova n’kumene kwandithandiza kukhala munthu wabwino komanso nzika yodalirika ya dziko la Russia. Ndikuthokoza Mulungu chifukwa wandithandiza kuti banja [langa] lisathe komanso kuti ndisinthe makhalidwe omwe ndinali nawo. Ndikuthokozanso Yehova pondithandiza kuti moyo wanga ukhale watanthauzo ndiponso kuti ndikhale ndi chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo. Chinthu chamtengo wapatali chimene ndapeza ndi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu. Ndimasangalala kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngakhale kuti ndikuimbidwa mlandu wabodza.”
A Levchuk ananena kuti: “Ndikuona kuti pa nthawi yonseyi, ndayesetsa kukhala wodekha chifukwa choti Yehova ali ku mbali yanga ndipo inenso ndili ku mbali yake. Kaya khoti ligamula zotani, koma chofunika kwambiri kwa ine ndi mmene Yehova amandionera. Kwa ine zilibe kanthu kuti ndili kuti, koma ndipitirizabe kusonyeza makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu monga chikondi, chimwemwe, kukoma mtima, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”