Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Sergey Ledenyov ndi mkazi wake Anna

NOVEMBER 20, 2020
RUSSIA

M’bale Sergey Ledenyov Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 6 ku Russia

M’bale Sergey Ledenyov Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 6 ku Russia

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 24 November 2020, * Khoti la m’Mzinda wa Petropavlovsk-Kamchatskiy m’Chigawo cha Kamchatka lidzapereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Sergey Ledenyov. M’baleyu akhoza kugamulidwa kuti akakhale kundende zaka 6.

Zokhudza M’baleyu

Sergey Ledenyov

  • Chaka chobadwa: 1974 (Ku Ossora, m’Chigawo cha Kamchatka)

  • Mbiri yake: Anabadwa ana 6 m’banja lawo. Amakonda kujambula zinthu pamanja komanso ndi kamera. Amagwira ntchito yomanga ndiponso kuika matailosi. Poyamba ankaona kuti Baibulo siligwirizana ndi sayansi ndipo ndi lachikale koma ataphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova maganizo amenewa anatheratu. Mu 2017 anakwatirana ndi Anna. Anna akunena kuti Sergey anasintha n’kukhala munthu wodekha komanso mwamuna wachikondi atayamba kugwiritsa ntchito zimene ankaphunzira m’Baibulo.

Mlandu Wake

Pa 2 December 2018, apolisi okhala ndi zida komanso ovala zophimba kunkhope anathyola ndi kulowa m’nyumba ya M’bale Ledenyov ku Petropavlovsk-Kamchatskiy. M’baleyu amaimbidwa mlandu mogwirizana ndi Gawo 282.2 la Buku la Malamulo a Zaupandu ku Russia. Khoti linayamba kuzenga mlanduwu pa 28 November 2019.

Pa 12 December 2019, Khoti la m’Mzinda wa Petropavlovsk-Kamchatskiy m’Chigawo cha Kamchatka linabwezera mlanduwu kwa woimira boma. Kawirikawiri zimenezi zimachitika ngati khoti lapeza mavuto aakulu pa mlandu umene munthu akuimbidwa monga kusowa maumboni okwanira. Komabe pa 4 February 2020 khoti lina lalikulu linasintha chigamulochi ndipo linayambiranso kuzenga mlanduwu. Kenako, pa nthawi imene mlanduwu unkazengedwa, apolisi anafunsa mafunso mkazi wa M’bale Ledenyov ndi mlongo wina ndi cholinga chofuna kuwapanikiza kuti anene maumboni abodza okhudza M’bale Ledenyov. Mlongo Ledenyov ndi mlongo winayo anakanitsitsa kuchita zomwe apolisi ankafunazo.

Achibale a M’bale Ledenyov omwe si Mboni sakumvetsa chifukwa chimene m’bale wawo akumuzunzira chifukwa cha chikhulupiriro chake.

Tikupempherera M’bale ndi Mlongo Ledenyov pamene akudikira chigamulo cha mlanduwu. Tikukhulupirira ndi mtima wonse kuti mzimu wa Yehova ukukhazikika pa iwo.—1 Petulo 4:14.

^ ndime 3 Detili likhoza kusinthidwa.