Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: M’bale Aleksandr Shamov ndi mkazi wake Nadezhda; M’bale Andrey Shchepin ndi mkazi wake Ksenia; M’bale Yevgeniy Udintsev ndi mkazi wake Elizaveta

APRIL 29, 2021
RUSSIA

M’bale Shamov, M’bale Shchepin, ndi M’bale Udintsev Akupitiriza Kukhalabe Okhulupirika Pamene Akuimbidwa Mlandu Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

M’bale Shamov, M’bale Shchepin, ndi M’bale Udintsev Akupitiriza Kukhalabe Okhulupirika Pamene Akuimbidwa Mlandu Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

MMENE ZINTHU ZILILI PANOPA | Khoti Lina ku Russia Lalipiritsa Chindapusa M’bale Shamov, M’bale Shchepin, ndi M’bale Udintsev

Pa 19 July 2021, Khoti la m’Boma la Leninskiy m’chigawo cha Kirov linagamula kuti M’bale Aleksandr Shamov, M’bale Andrey Shchepin, ndi M’bale Yevgeniy Udintsev ndi olakwa ndipo linalamula kuti a Shamov apereke ndalama zokwana marubo 420,000 (Madola 5,618 a ku United States); a Shchepin apereke marupo 500,000 (Madola 6,688 a ku United States) komanso a Udintsev apereke marupo 200,000 (Madola 2,675 a ku United States). Abalewa sakufunika kukakhala kundende.

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la m’Boma la Leninskiy, M’chigawo cha Kirov posachedwapa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Aleksandr Shamov, M’bale Andrey Shchepin komanso M’bale Yevgeniy Udintsev. a

Zokhudza Abalewa

Aleksandr Shamov

  • Chaka chobadwa: 1960 (ku Komarovo, M’chigawo cha Kirov)

  • Mbiri yake: M’banja mwawo muli ana 6. Makolo ake anamwalira ali wamng’ono. Ankalima ku famu yakwawo kuyambira ali ndi zaka 6. Atamaliza maphunziro a ku koleji anayamba kugwira ntchito yokonza ma TV. Mu 1986 anakwatira Nadezhda. Ali ndi mwana wamkazi wamkulu. Anamuchita opaleshoni ya mtima n’kuchira, ndipo panopa amalandira nawo ndalama zimene zimaperekedwa kwa anthu amene sakutha kugwira ntchito chifukwa vuto la thanzi lawo. Cha m’ma 1990, iye limodzi ndi mkazi wake Nadezhda anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Mu 2000 anabatizidwa

Andrey Shchepin

  • Chaka chobadwa: 1991 (ku Korolev, M’chigawo cha Moscow)

  • Mbiri yake: Anaphunzira choonadi kuchokera kwa makolo ake. Mu 2015 anakwatira Ksenia. Ndi katswiri wa zomangamanga. Anabatizidwa mu 2010

Yevgeniy Udintsev

  • Chaka chobadwa: 1949 (ku Kirov)

  • Mbiri yake: Ali mwana anali ndi vuto lalikulu la mtima. Ndi katswiri wa zomangamanga komanso ali ndi luso lowotcherera. Mu 1970 Anakwatira Elizaveta. Onse anaphunzira choonadi kwa mchemwali wake wa Elizaveta mu 1991. Kukonda Yehova kunamuthandiza kuti asiye kusuta komanso kuledzera. Anabatizidwa mu 1996

Mlandu Wawo

Pa 26 March 2019, akuluakulu a boma a ku Russia anakachita chipikisheni m’nyumba za abale 12 a Mboni. Akuluakuluwa anafufuzanso mosamala zokhudza a Mboni ndipo pambuyo pake anayamba kuimba mlandu M’bale Aleksandr, M’bale Andrey, komanso M’bale Yevgeniy. Andrey anatsekeredwa m’ndende kwa masiku awiri. Oweruza milanduwo ananena kuti kulambira kumene abalewa amachita ndi “koopsa.” Abalewa akuimbidwa milandu monga kuwerenga Baibulo komanso kuimba nyimbo za Ufumu

Kuti akwanitse kupirira chizunzochi, abalewa akupitirizabe kudalira kwambiri Yehova, gulu lake komanso Baibulo. Mwachitsanzo, Aleksandr amapeza mphamvu pa zitsanzo za “mtambo wa mboni waukulu” zotchulidwa muchaputala 12 cha Aheberi. Iye anati: “Kalelo atumiki a Mulungu anazindikira kuti kukhala ndi chikhulupiriro kumafuna kulimba mtima komanso kupirira. Zinthu zikayamba kundivuta, ndimaganizira zitsanzo zawo. Iwo anazunzidwa kwambiri komanso kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Zimenezi zimandithandiza kuti ndipitirizebe ‘kumenya nkhondo yachikhulupiriro.’”​—Yuda 3.

Andrey amalimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani za a Mboni omwe anakhalabe okhulupirika pamene ankazunzidwa ndi chipani cha Nazi ku Germany komanso ku Soviet Union. Iye anati: “Ndimasirira kwambiri kulimba mtima kwawo.” Andrey amachitanso chidwi kwambiri ndi mmene Yehova anayankhira mapemphero awo komanso kuwapatsa mphoto chifukwa chokhalabe okhulupirika. Zimenezi zinamuchititsa kuti azitchula zinthu zenizeni zimene akufuna akamapemphera kwa Yehova. Iye anafotokoza kuti: “Ndimapempha kuti andithandize kukhala wolimba mtima, inde kulimba mtima, ndipo ndibwerezanso, kukhala wolimba mtima. . . . Tikudziwa kuti tikukhala m’nthawi yapadera kwambiri. Zimenezi zimatipatsa mwayi wochita utumiki, wokhala ndi maluso komanso wodalira kwambiri Yehova.”

Tikupempherera abalewa limodzi ndi mabanja awo. Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuwatonthoza komanso ‘kuwalimbikitsa muntchito yabwino iliyonse ndiponso m’mawu.’​—2 Atesalonika 2:17.

a N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo