JULY 5, 2019
RUSSIA
M’bale Stupnikov Wamasulidwa pa Ukaidi Wosachoka Panyumba
Pa 2 July, 2019, khoti la ku Krasnoyarsk m’dziko la Russia linagamula kuti m’bale Andrey Stupnikov amasulidwe pa ukaidi wosachoka panyumba. Ngakhale kuti panopa sali pa ukaidi wosachoka panyumba, akumuganizirabe kuti anapalamula mlandu.
Pa 3 July, 2018, M’bale ndi Mlongo Stupnikov ankaonetsa matikiti awo asanakwere ndege ya m’mamawa pabwalo la ndege la Krasnoyarsk International Airport ku Yemelyanovo m’dziko la Russia. Kenako anthu awiri oimira gulu lina loona za chitetezo (Federal Security Service) anafika ndipo anamanga M’bale Stupnikov. M’baleyu anakhala m’ndende miyezi 8 asanazengedwe mlandu ndipo kenako chakumapeto kwa February 2019, anauzidwa kuti akhale paukaidi wosachoka panyumba.
Zimene M’bale Stupnikov ananena zikusonyeza kuti waphunzira zambiri zokhudza iyeyo komanso ubwenzi wake ndi Yehova m’chaka chapitachi. Iye anati: “[Ine ndi Olga] takhala a Mboni kwa zaka zambiri koma sitinadzimvepo kuti tili pafupi kwambiri ndi Yehova ngati mmene tamvera pa nthawiyi. M’nthawi zovuta kwambiri, ndinkaona kuti Atate wathu anali nafe komanso ankatithandiza, ndipo ndikuona kuti akupitirizabe kuchita zimenezi. Zimandidabwitsa kuona mmene Yehova wakhalira nane pafupi kwambiri komanso mmene wayankhira mapemphero anga mwamsanga.”
Pomaliza, M’bale Stupnikov anati: “Kuposa mmene ndinkaonera m’mbuyomu, panopa ndikukhulupirira kuti Atate wanga amadziwa komanso amamvetsa mmene ndikumvera. Zimene ndakumana nazozi zandithandiza kuti ndizimudalira kwambiri komanso kuti ndisamadandaule kwambiri ndi kuzunzidwa. Kutaya ubwenzi wanga ndi Yehova n’kumene kuli koopsa kwambiri. Panopa ndili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova angatithandize kuthana ndi vuto lililonse.”
Chiwerengero cha abale ndi alongo athu omwe akumangidwa ku Russia chikupitirizabe kukwera. Pofika pa 1 July, akuluakulu a boma anali kufufuza milandu ya abale ndi alongo okwana 217. Pa milandu yochepa, akuluakulu a boma la Russia anachepetsa zilango zomwe abale athu ena anapatsidwa. Komabe, sitidalira makhoti a anthu kapena akuluakulu a boma, m’malomwake tipitirizabe kudalira Yehova. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kulimbitsa ndiponso kuteteza abale athu onse ku Russia.—Salimo 28:7.