Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Moskalenko yemwe watulutsidwa m’ndende, ali panja pa khoti

SEPTEMBER 4, 2019
RUSSIA

M’bale Valeriy Moskalenko Watulutsidwa M’ndende

M’bale Valeriy Moskalenko Watulutsidwa M’ndende

Pa 2 September, 2019, khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy ku Khabarovsk m’dziko la Russia, linagamula kuti M’bale Valeriy Moskalenko agwire ntchito yothandiza m’dera lake kwa zaka ziwiri ndi miyezi iwiri, komanso kuti kwa miyezi ina 6 aziyang’aniridwa monga munthu yemwe anapalamula mlandu. M’baleyu sakufunikanso kuti akhale m’ndende kwa nthawi ina yowonjezera.

Khoti litangolengeza za chigamulochi, M’bale Moskalenko anatulutsidwa m’ndende ndipo banja lake komanso anzake anasangalala kwambiri. M’baleyu anali atakhala m’ndende kuyambira pa 2 August, 2018. Asanamangidwe, M’bale Moskalenko ankagwira ntchito monga wothandizira kondakitala wa sitima yapamtunda ndipo ankathandizanso mayi ake omwe akudwala. Pa nthawi yomwe aziyang’aniridwa, m’baleyu sakuloledwa kutuluka mumzinda wa Khabarovsk ndipo mwezi uliwonse ayenera kumakaonekera kupolisi kuti azikatsimikizira kuti sakuchita chilichonse chosemphana ndi malamulo.

Pamene ankayankhula mawu ake omaliza m’khoti pa 30 August, mwa zina, M’bale Moskalenko anati: “Sindingachite zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna zomwe zinafotokozedwa momveka bwino m’Baibulo. Ndipo kaya nditakakamizidwa bwanji kapena kupatsidwa chilango chotani, ngakhalenso kugamulidwa kuti ndiphedwe, ndikulengeza kuti sindidzasiya Mlengi wachilengedwe chonse, yemwenso ndi wamphamvuyonse, Yehova Mulungu.”

A Yaroslav Sivulskiy omwe ndi oimira bungwe la European Association of Jehovah’s Witnesses anati: “Ngakhale kuti sitikugwirizana ndi chigamulo choti ndi wolakwa, tikusangalala kuti M’bale Moskalenko abwerera kunyumba.”

Kuwonjezera pa M’bale Moskalenko, abale enanso 7 m’dera la Khabarovsk akuyembekezera kumva zigamulo za milandu yawo.

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa choti M’bale Moskalenko anakhalabe ndi chikhulupiriro cholimba pa nthawi yomwe anali m’ndende. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kupereka mphamvu kwa abale ndi alongo onse omwe akupirira chizunzo chifukwa cha mfundo za m’Baibulo zomwe amakhulupirira.—Yesaya 40:31.