Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Vitaliy Ilinykh

MAY 10, 2021
RUSSIA

M’bale Vitaliy Ilinykh Amalimbikitsidwa ndi Chitsanzo cha Ena

M’bale Vitaliy Ilinykh Amalimbikitsidwa ndi Chitsanzo cha Ena

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la M’boma la Ussuriyskiy M’chigawo cha Primorye, posachedwapa likuyembekezereka kulengeza tsiku limene lidzapereke chigamulo pa mlandu wa M’bale Vitaliy Ilinyk. *

Zokhudza M’baleyu

Vitaliy Ilinykh

  • Chaka chobadwa: 1974 (Ku Ussuriyskiy M’chigawo cha Primorye)

  • Mbiri yake: Anamaliza maphunziro a ntchito ya polisi ndipo ankagwira ntchito mu dipatimenti yoona za m’dziko. Nthawi zonse ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani anthu amamwalira komanso zimene zimachitika munthu akamwalira. Anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova cha m’ma 1990 ndipo anabatizidwa mu 1999. Panopa amagwira ntchito yoyeretsa mu msewu. Anakwatirana ndi Irina mu 2006.

Mlandu Wake

Mu February 2019, apolisi anakachita chipikisheni ku nyumba ya M’bale Vitaliy Ilinykh ngati mbali ya mlandu umene abale ena ankazengedwa mu mzinda wa Spassk-Dalniy. Pa 18 September 2019, akuluakulu a boma la Russia anayamba kufufuza M’bale Vitaliy. Pa 23 October 2019, apolisi anakachitanso chipikisheni ku nyumba kwa m’baleyu ndipo panthawiyi anamumanga n’kukamuika ku malo osungirako anthu oimbidwa mlandu komwe anakhalako masiku awiri. Ali ku malowa, M’bale Vitaliy anapemphera kwa Yehova. Iye nati: “Nditapemphera, ndinasiya kuchita mantha ndipo mtima wanga unali m’malo.”

Pamene m’baleyu ankamutulutsa, anamuuza kuti sakuloledwa kumakayenda kupita kwina. Mayi ake omwe ndi Mlongo Olga Opaleva, nawonso akuwazenga mlandu koma wosiyana ndi wa m’baleyu.

M’bale Vitaliy waphunzira zambiri kuchokera pa zimene wakumana nazo. Iye anati: “M’mbuyomu ndinkadziwa kuti Yehova salola kuti tiyesedwe mpaka kufika poti sitingapirire. Panopa ndaona zimenezi zikuchitika pa moyo wanga. Ndaona kuti zinthu zikamafika pothina pa moyo wathu m’pamenenso timadalira kwambiri Yehova. Yehova ndiye Wondiwumba ndipo akalola kuti ndikumane ndi mayesero ena ake pa moyo wanga, adzandithandiza kupirira ndipo akhoza kugwiritsa ntchito mayeserowo kuti iye andiumbe mmene akufunira. Ndikaona kuti sindingakwanitse kuwapirira mayeserowo, ndimaona kuti imeneyi ndi nthawi yabwino yoti ndipemphe Yehova kuti andipatse ‘mphamvu yoposa yachibadwa.’”​—2 Akorinto 4:7.

Mwachibadwa, Vitaliy ndi munthu wamanyazi, koma panopa amalimba mtima akamaganizira lemba la 1 Petulo 5:9. Kuwonjezera pamenepa, akumalimbikitsidwanso ndi chitsanzo cha abale ndi alongo ambirimbiri a ku Russia omwe akukwanitsa kupirira chizunzo. M’bale Vitaliy analankhula molimba mtima kuti: “Zilizonse zimene Yehova alole akhoti kugamula pa mlandu wangawu, . . . ukhala mwayi wochitira umboni kwa akuluakulu aboma m’masiku otsiriza ano.”

Mofanana ndi M’bale Vitaliy, tonsefe timalimbikitsidwa ndi zitsanzo za abale ndi alongo omwe ali ndi chikhulupiriro champhamvu komanso olimba mtima. Tikupitiriza kuthokoza Yehova chifukwa chotipatsa ‘chilichonse chabwino kuti tichite chifuniro chake.’​—Aheberi 13:20, 21.

^ N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo..