Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Vladimir Alushkin ndi mkazi wake Tatyana

SEPTEMBER 16, 2020
RUSSIA

M’bale Vladimir Alushkin Sakufunika Kupitanso Kundende

M’bale Vladimir Alushkin Sakufunika Kupitanso Kundende

Pa 16 September 2020, khoti la m’chigawo cha Penza linapereka chigamulo chake pa mlandu wa apilo wokhudza M’bale Vladimir Alushkin, Vladimir Kulyasov, Andrey Magliv, ndi Denis Timoshin ndiponso Mlongo Tatyana Alushkina ndi Galiya Olkhova. Khotili linachepetsa nthawi yokhala kundende imene M’bale Alushkin anapatsidwa, kuchoka pa zaka 6 kufika pa zaka 4. Ndipo m’malo mokhala kundende anangopatsidwa malamulo oti azitsatira pa zaka zimenezi. Ndife osangalala kuti m’baleyu sakufunika kupitanso kundende. Chigamulo cha anthu enawa choti azingotsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo sichinasinthe.