Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Tatyana Alushkina akumuhaga mwamuna wake, Vladimir, atatulutsidwa m’ndende

APRIL 10, 2020
RUSSIA

M’bale Vladimir Alushkin Watulutsidwa M’ndende

M’bale Vladimir Alushkin Watulutsidwa M’ndende

M’bale Vladimir Alushkin anatulutsidwa m’ndende pa 30 March 2020, ndipo panopa ali limodzi ndi mkazi wake.

M’baleyu anatulutsidwa potengera chigamulo chomwe khoti la mumzinda wa Penza linapereka pa 25 March, chomwenso chinatchulidwa m’nkhani ina ya m’mbuyomu. Chigamulochi chinasintha zimene khoti linagamula pa milandu ya abale awa: Vladimir Alushkin, Vladimir Kulyasov, Andrey Magliv, ndi Denis Timoshin. Komanso alongo awa: Tatyana Alushkina ndi Galiya Olkhova. Khoti la mumzinda wa Penza linapempha khoti lomwe linaweruza koyamba milandu ya abale ndi alongowa, kuti lisankhe woweruza wina ndipo azengenso milanduyi. Pakali pano, abale ndi alongo onse 6 akutsatira ziletso zomwe khoti linawapatsa pa nkhani zokhudza kuyenda ndi zinthu zina.

Ngakhale kuti tikusangalala kuti M’bale Alushkin anatulutsidwa, patangodutsa masiku awiri, kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Russia, m’bale wathu wina anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Pamene abale ndi alongo athu ku Russia akuimbidwabe milandu popanda zifukwa zomveka, n’zosakayikitsa kuti akukumbukira ndiponso kudalira mawu a pa Nahumu 1:7 omwe amati: “Yehova ndi wabwino ndipo ndi malo achitetezo pa tsiku la nsautso. Amadziwa amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.”