Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuyambira kumanzere kupita kumanja: M’bale Vladimir Chesnokov, Vladimir Dutkin, ndi Valeriy Yakovlev

7 JANUARY, 2022
RUSSIA

M’bale Vladimir Chesnokov, Vladimir Dutkin ndi M’bale Valeriy Yakovlev, Anazengedwa Mlandu Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

M’bale Vladimir Chesnokov, Vladimir Dutkin ndi M’bale Valeriy Yakovlev, Anazengedwa Mlandu Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. Khothi la m’boma la Kalininskiy lomwe lili mumzinda wa Cheboksary, posachedwa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Vladimir Chesnokov, Vladimir Dutkin ndi M’bale Valeriy Yakovlev. Loya wa boma sananene chilango chimene akufuna kuti abalewa apatsidwe

  2. 7 June, 2021

    M’bale Vladimir Chesnokov ndi Valeriy Yakovlev nawonso anaphatikizidwa pa mlanduwo

  3. 30 December, 2020

    A Vladimir Dutkin anawapeza ndi mlandu ndipo anawalamula kuti asamayende kupita malo ena

  4. 25 November, 2020

    Apolisi anayamba kufufuza mlandu wa a Vladimir Dutkin ndipo kenako anakafufuza zinthu m’nyumba mwawo. Pambuyo pake anawatenga kuti akawafunse mafunso

Zokhudza M’baleyu

Kuwerenga ndi kuganizira mozama Mawu ouziridwa a Mulungu, kwathandiza abale ndi alongo athu kupirira mavuto omwe amakumana nawo tsiku ndi tsiku. Zawathandizanso kuona kuti Yehova ‘amawabisa m’malo ake otetezeka.’​—Salimo 27:5.