Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Vladimir Filippov ndi mkazi wake, Lyubov

26 JANUARY 2021
RUSSIA

M’bale Vladimir Filippov Wazaka 77 Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 6 ndi Hafu

M’bale Vladimir Filippov Wazaka 77 Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale Kundende Zaka 6 ndi Hafu

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 27 January 2021, a Khoti la m’Boma la Nadezhdinskiy m’Chigawo cha Primorskiy lidzalengeza chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Vladimir Filippov. Iye akhoza kugamulidwa kuti akakhale m’ndende zaka 6 ndi hafu.

Zokhudza M’baleyu

Vladimir Filippov

  • Chaka chobadwa: 1943 (Ku Oktyabrskiy, M’chigawo cha Novosibirsk)

  • Mbiri yawo: A Filippov atangobadwa kumene, bambo awo anaphedwa pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Mu 1964 anamaliza maphunziro awo pa sukulu ina yopanga zida zankhondo ku Tomsk ndipo anakhala mkulu wa asilikali. M’chaka cha 1967 anakwatirana ndi a Lyubov. Anagwira ntchitoyi kwa zaka 27 kenako anapuma pa ntchito

    Anayamba kuphunzira Baibulo mu 1994 patangopita nthawi yochepa akazi awo atayamba kuphunzira. Kenako onse anabatizidwa mu 1995

Mlandu Wawo

Mu August 2017, apolisi anayamba kujambula mwachinsinsi mavidiyo ndi mawu a M’bale Filippov ndi abale ena ku Razdolnoye. Kwa miyezi ndithu, apolisiwa ankangojambula mwachinsinsi M’bale Filippov akamakamba nkhani pamisonkhano komanso akamauzako ena mfundo za m’Baibulo.

Pa 19 July 2018, apolisi a gulu la FSB anathyola n’kulowa m’nyumba ya M’bale Filippov atanyamula zida komanso atavala zotchinga nkhope. Apolisiwa anamenya mbama a Filippov ndi kuwagoneka pansi, kuwamanga nyakula kenako anayamba kupanga chipikisheni m’nyumba yawo. Pa nthawiyi a Filippov n’kuti ali ndi zaka 75. Apolisi anabweranso kudzapanga chipikisheni m’nyumba ya M’bale Filippov mu August 2019 komanso mu January 2020. A Filippov anayamba kuimbidwa mlandu apolisi atakapanga chipikisheni kachiwiri kunyumba kwawo.

Tikupempha kuti Yehova apitirize kupatsa abale ndi alongo athu mphamvu kuti ziwathandize kukhalabe okhulupirika komanso achimwemwe.​—Yesaya 40:29, 31.

a Detili likhoza kusinthidwa.