Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Semyon Baybak

NOVEMBER 25, 2020
RUSSIA

M’bale Wachinyamata Dzina Lake Semyon Baybak Akaonekera Kukhoti Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

M’bale Wachinyamata Dzina Lake Semyon Baybak Akaonekera Kukhoti Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 18 December 2020, Khoti la m’Boma la Leninskiy M’chigawo cha Rostov-on-Don lidzalengeza chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Semyon Baybak. Woimira boma pa mlanduwu wapempha khoti kuti Semyon apatsidwe chigamulo choti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwa zaka 4.

Zokhudza M’baleyu

Semyon Baybak

  • Chaka chobadwa: 1997 (Ku Rostov-on-Don)

  • Mbiri yake: Ali ndi mchimwene komanso mchemwali wake omwe ndi aakulu kwa iyeyo. Anaphunzira chinenero cha Chitchainizi ndipo amagwira ntchito yophunzitsa anthu chinenerochi. Amakonda kuwerenga komanso kulemba ndakatulo

  • Makolo ake anamuphunzitsa za Yehova ali wamng’ono. Pamene ankakula, anaphunzira malangizo anzeru ochokera m’Baibulo ndipo anasankha kuti aziwatsatira. Iye anakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira. Kuyambira mu 2015 mpaka mu 2017, ankagwira ntchito ya ukilinala yomwe ndi yosakhudzana ndi usilikali pachipatala china cha ana

Mlandu Wake

Pa 22 May 2019, apolisi ogwira ntchito yothana ndi anthu ochita zinthu zoopsa anakachita zipikisheni m’nyumba 13 za a Mboni ku Rostov-on-Don. Patapita milungu iwiri, pa 6 June 2019, apolisi anamutsegulira mlandu. Kenako anamumanga n’kumutsekera muselo yongoyembekezera ndipo khoti linagamula kuti akhale pa ukaidi wosachoka panyumba. Poyamba anauzidwa kuti agwira ukaidiwu kwa milungu 8 komano nthawiyi anaiwonjezera kuwirikiza maulendo 7.

Poyamba apolisiwo ananena kuti Semyon anapezeka ndi “milandu” chifukwa chochita nawo misonkhano yachipembedzo chake komanso kuuza ena zimene anaphunzira kuchokera m’Baibulo. Pomwe mu November 2019, ananenanso kuti anapezeka ndi mlandu wopereka ndalama zothandizira gulu “loopsa.”

Ngakhale kuti abale ndi alongo athu akuzunzidwabe ku Russia, tikudziwa kuti Yehova yemwe ndi “Mulungu wamtendere,” apitirizabe kuwapatsa zinthu zonse zimene akufunikira ‘kuti achite chifuniro chake.’—Aheberi 13:20, 21.

Detili likhoza kusinthidwa.