Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Yevgeniy Golik ali panja pa khoti mu December 2020

JANUARY 21, 2021
RUSSIA

M’bale Yevgeniy Golik Wagamulidwa Kuti Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

M’bale Yevgeniy Golik Wagamulidwa Kuti Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 20 January 2021, Khoti la m’Boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia linagamula kuti M’bale Yevgeniy Golik ndi wolakwa. Khotili linalamula kuti m’baleyu azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake kwa zaka ziwiri ndi hafu. Panopa m’baleyu sakuyenera kukakhala kundende. Iye apanga apilo chigamulochi.

Zokhudza M’baleyu

Yevgeniy Golik

  • Chaka chobadwa: 1975 (Ku Birobidzhan, M’dera Loima Palokha la Ayuda ku Russia)

  • Mbiri yake: Anaphunzira ntchito yowotcherera zinthu. Amagwira ntchito yoyang’anira komanso kuyendetsa mashini. Asanakhale wa Mboni za Yehova ankagwira ntchito yausilikali ku Russia

    Mayi awo ndi amene nawaphunzitsa choonadi. Anapeza mayankho okhudza cholinga cha moyo. Mfundo za m’Baibulo zinawathandizanso kuti azikonda kwambiri anthu ena

Mlandu Wake

M’mamawa pa 17 May 2019, apolisi 150 a gulu la chitetezo (FSB) anapanga chipikisheni m’nyumba 9 za a Mboni za Yehova mu mzinda wa Birobidzhan womwe uli Chakummawa m’dziko la Russia. Chipikisheni chimene apolisiwa anapanga anachitchula kuti “Tsiku la Chiweruzo.” Apolisi a ku Birobidzhan anatsegulira milandu M’bale Yevgeniy Golik komanso abale ndi alongo enanso 21 ochokera m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia. Mlandu wa M’bale Golik unayamba kuzengedwa pa 29 January 2020.

Oimira boma pamlanduwu anapereka umboni womwe unaphatikizapo ma mavidiyo osonyeza M’bale Golik akuwerenga Baibulo ndi mabuku athu enanso ambiri.

Si zophweka kupirira zinthu zopanda chilungamo ngati zimenezi. Komabe, M’bale Golik akunena kuti: “Kuphunzira Baibulo ndi kupemphera kwa Yehova nthawi zonse kwandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri zokhudza Yehova osati mavuto anga.” Mfundo zothandiza zimene ndimapeza m’Mawu a Mulungu zimandithandiza kukhala wosangalala ndipo zimandichititsa kuti ndiziuzako ena zomwe ndaphunzirazo.

Kuganizira kwambiri lemba la Salimo 23:4 kwamuthandiza kwambiri m’baleyu. Iye akuti: “[Lemba limeneli] landithandiza kwambiri kukhala wolimba mtima komanso kukhala wosangalala popirira mavuto. Ngakhale pamene moyo wathu uli pa ngozi, timadziwa kuti nthawi zonse Yehova amakhala nafe.”

A Mboni za Yehova ena anamuthandizanso kwambiri. M’baleyu akunena kuti: “Mlandu wanga utayamba kuzengedwa abale ndi alongo anabwera kukhoti ndipo zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri. Komanso Yehova anandipatsa mkazi wabwino kwambiri yemwe anandithandiza pa nthawi yovutayi. Ndimakhala wosangalala nthawi zonse. Ndili ndi Mawu a Mulungu, chakudya chokwanira komanso ndikuthandizidwa m’njira zambiri.”

M’bale Golik ndi wotsimikiza mtima kuti adzakhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Pofuna kuthandiza anthu amene sanazunzidwepo ngati iyeyo kukonzekera mayesero, m’baleyu akunena kuti: “Muziphunzira nyimbo [za Ufumu], muzidziphunzitsa kukonda adani anu komanso mudziphunzitse kutumikira Mulungu mwachimwemwe m’nthawi zabwino ndi zovuta zomwe.”

Tonsefe tipitirize kuphunzira zambiri kwa abale ndi alongo athu a ku Russia. Panopa Yehova akuwathandiza kukhala olimba ngakhale akukumana ndi mayesero. Ifenso adzatilimbitsa.—Salimo 29:11.