Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Yevgeniy Spirin ali muselo ya m’khoti

JULY 9, 2020
RUSSIA

M’bale Yevgeniy Spirin Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale M’ndende Zaka 7 ku Russia

M’bale Yevgeniy Spirin Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale M’ndende Zaka 7 ku Russia

Pa 14 July 2020, khoti la mumzinda wa Furmanovsky M’chigawo cha Ivanovo, lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Yevgeniy Spirin. Woimira boma pa mlanduwu wapempha khoti kuti ligamule kuti M’bale Spirin akakhale kundende zaka 7.

M’bale Spirin ali ndi zaka 34 ndipo akuimbidwa mlandu woyendetsa ntchito za gulu lomwe boma la Russia limaona kuti limachita “zinthu zoopsa.” Mlanduwu unayamba pa 21 January 2019 ndipo anauyambitsa ndi wapolisi wofufuza milandu wagulu lachitetezo la FSB m’chigawocho. Patapita masiku 6, a FSB anakathyola ndi kulowa m’nyumba ya M’bale Spirin ndi mkazi wake Natalya. Kenako khoti la m’boma la Oktyabrsky m’chigawo cha Ivanovo linagamula kuti M’bale Spirin aikidwe m’ndende kwa miyezi yosachepera iwiri poyembekezera kumuzenga mlandu, chifukwa chakuti ndi wa Mboni za Yehova basi. Pambuyo pake anadzamuonjezera nthawi yoti akhale m’ndende.

Atakhala m’ndende kwa masiku 160, m’baleyu anatulutsidwa pa 5 July 2019 n’kupatsidwa chilango choti akakhale pa ukaidi wapakhomo. Pa 18 December  2019, khoti la m’boma la Oktyabrsky m’chigawo cha Ivanovo linagamula kuti M’bale Spirin amasulidwe pa ukaidi wapakhomo ngakhale kuti amene ankafufuza za mlandu wake sanagwirizane nazo. Khotili silinaonjezerenso malamulo ena oti M’baleyu aziwatsatira.

Tikupemphera ndi kukhulupirira kuti Atate wathu wakumwamba Yehova, apitiriza kukhala ndi abale athu onse omwe akuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo ku Russia.—1 Petulo 4:14.