Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 23, 2020
RUSSIA

M’bale Yuriy Zalipayev Akhoza Kukakhala Kundende Zaka Ziwiri ku Russia

M’bale Yuriy Zalipayev Akhoza Kukakhala Kundende Zaka Ziwiri ku Russia

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 7 October 2020, * Khoti la m’Boma la Mayskiy ku Kabardino-Balkarian Republic lidzapereka chigamulo chake pa mlandu wokhudzana ndi M’bale Yuriy Zalipayev. M’baleyu atha kugamulidwa kuti akakhale kundende zaka ziwiri.

Zokhudza M’baleyu

Yuriy Zalipayev

  • Chaka chobadwa: 1962 (Ku Samara)

  • Mbiri yake: Wakhala akugwira ntchito yowotcherera zitsulo ndi kuyendetsa thiraki. Amakonda kulemba ndakatulo komanso kukwera mapiri

  • Mu 1983 anakwatira a Natalia omwe ankaphunzira nawo kalasi imodzi pa nthawi imene anali ana. Patadutsa zaka 10 onse anayamba kuphunzira Baibulo. Ali ndi ana atatu. Onse amatumikira Yehova limodzi ndi achibale awo ena.

Mlandu Wake

Pa 20 August 2016, apolisi anathyola n’kulowa mu Nyumba ya Ufumu ku Mayskiy ndipo anaikamo ena mwa mabuku athu omwe analetsedwa chifukwa boma limati ndi “oopsa.” Ngakhale kuti popereka umboni abale anali ndi vidiyo yosonyeza kuti apolisiwo ndi amene anachita kuika mabukuwo, khoti linanena kuti abalewo aphwanya malamulo ndipo linawalipiritsa chindapusa cha ndalama zokwana madola 2,634 a ku America. Patadutsa miyezi ingapo, M’bale Zalipayev anayamba kuimbidwa mlandu potengera zomwe zinachitika pa 20 August.

Oimira boma ananena kuti M’bale Zalipayev amagawira ena mabuku oletsedwa ndipo amalimbikitsa a Mboni za Yehova ena kuchitira nkhanza anthu a zipembedzo zina. Kuchita zimenezi n’kosavomerezeka malinga ndi lamulo lina lolimbana ndi zinthu zoopsa.—Mbali Yoyamba ya Gawo 280 la Buku la Malamulo a Zaupandu ku Russia.

Khoti linayamba kuzenga mlanduwu pa 21 June 2020. Pa nthawi yonse imene mlanduwu unkazengedwa, mboni za boma zinkakonda kufotokoza zinthu zosagwirizana kapenanso zinthu zosonyeza kuti palibe umboni wogwirika wa mlanduwo. Mwachitsanzo, mlanduwu uli mkati, mboni za boma zomwe zinanena kuti zinamva M’bale Zalipayev akulimbikitsa anthu ena kuchita zinthu zankhanza kunalibe kumisonkhanoyo. Komanso mboni zina zinaulula kuti mabuku oletsedwa omwe anapezeka m’Nyumba ya Ufumu anaikamo ndi apolisi.

Pamene M’bale Zalipayev akudikirira chigamulo cha mlandu wakewu, tikupemphera kuti iye limodzi ndi banja lake alimbikitsidwe ndi kupeza mtendere m’mawu a Davide akuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa. Mtima wanga umam’khulupirira. Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.”—Salimo 28:7.

^ ndime 3 Detili likhoza kusinthidwa