Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Galina Parkova

25 JANUARY 2021
RUSSIA

Mlongo Galina Parkova Akuyembekezera Kuweruzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake Pomwe Mwamuna Wake Ali Kale M’ndende

Mlongo Galina Parkova Akuyembekezera Kuweruzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake Pomwe Mwamuna Wake Ali Kale M’ndende

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la m’Boma la Leninskiy ku Rostov-on-Don, likuyembekezera kulengeza chigamulo chake posachedwapa pa mlandu wa Mlongo Galina Parkova. * Ngati mlongoyu angapezedwe wolakwa, oimira boma pamlanduwu apempha khoti kuti ligamule kuti azikatsatira malamulo ena ali kunyumba kwa zaka zitatu.

Zokhudza Mlongoyu

Galina Parkova

  • Chaka chobadwa: 1970 (Ku Kaltan)

  • Mbiri yake: Mu 1990, a Galina anakwatirana ndi a Aleksandr. Ali ndi ana aakazi atatu ndi zidzukulu ziwiri. Anaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo anabatizidwa mu 1995. Amakonda kuimba ndi kujambula

Mlandu Wawo

Apolisi anayamba kuimba mlandu Mlongo Galina pa 6 June 2019. Amuna awo a Aleksandr anali atamangidwa n’kukasungidwa m’ndende milungu ingapo a Galina asanayambe kuimbidwa mlanduwu.

A Galina akhala akuvutika kupeza zofunika pa moyo chifukwa chakuti amuna awo akusungidwa m’ndende. Komanso akuluakulu a boma anatseka khadi la kubanki la Mlongo Galina zomwe n’zovuta kuti azikatenga ndalama zawo kubanki. Izi zinachititsa kuti a Galina asiye kugwira ntchito yomwe ankagwira ndipo panopa amangogwira maganyu kuti azitha kupeza kangachepe.

Abale ndi alongo athu ku Russia ndi “anthu olungama amene amakumana ndi zinthu zimene amayenera kukumana nazo anthu oipa.” (Mlaliki 8:14) Komabe zitsanzo zawo pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro cholimba zikutithandiza kuti nafenso tisagwedezeke kaya tikumane ndi mayesero otani.

^ N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo.